LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 10/13 tsa. 2
  • Njila Zocitila Kulambila kwa Pabanja

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Njila Zocitila Kulambila kwa Pabanja
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Gwilitsilani Nchito Webusaiti ya jw.org mu Ulaliki—“Khala Bwenzi la Yehova”
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mfundo Yothandiza pa Kufufuza Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 10/13 tsa. 2

Njila Zocitila Kulambila kwa Pabanja

1. Kodi zolinga zina za zofalitsa zathu ndi ziti?

1 Zofalitsa zathu zambili zili ndi nkhani zimene colinga cake ndi kuthandiza ana aang’ono kuti azigwilizana ndi makolo ao ndi kutinso onse ayandikile kwa Yehova. (Deut. 6:6, 7) Kodi mungagwilitsile nchito bwanji zofalitsa zimene muli nazo pophunzitsa ana anu?

2. Kodi mungasankhe bwanji nkhani zoyenelelana ndi msinkhu wa ana anu?

2 Muzisintha: Mwana aliyense amakhala ndi zosoŵa zosiyana ndi za ana ena. (1 Akor. 13:11) Nanga kodi mungasankhe bwanji zofalitsa zimene zili ndi nkhani zogwilizana ndi msinkhu wa ana anu? Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi nkhani ziti zimene ana anga adzacita nazo cidwi? Kodi ndi zoculuka bwanji zimene angamve? Kodi angamvetsele kwa nthawi yaitali bwanji?’ Ngati muli ndi ana a zaka zitatu kapena zocepelapo, mungaphunzile nao nkhani zopezeka pa Webusaiti yathu pa cigawo cakuti “My Bible Lessons”. Mabanja ena amakonda nkhani za m’Baibo zopezeka pa cigawo cakuti “Teach Your Children.” Onaninso mbali zotsatilazi.

3. Kodi kulambila kwa pabanja kumatipatsa mwai wocita ciani?

3 Mabanja ena amakonzekela misonkhano ya mpingo pamodzi. Kucita zimenezi n’kwabwino koma si zokhazi zimene tingacite pa kulambila kwa pabanja. Kulambila kwathu kwa pabanja sikuyenela kukhala monga ndi msonkhano wampingo. Nthawi ya kulambila kwa pabanja iyenela kutipatsa mwai wolankhula zakukhosi. Ndi nthawi imene tingamaganizilepo kwambili pa zimene timaphunzila kuti tikhale ndi makambilano ogwila mtima. Mofanana ndi kufula uci mu mng’oma, pafunika luso kuti mudziŵe mmene mwana wanu amaonela zinthu ndipo kucita zimenezi n’kopindulitsa. Kulambila kwa pabanja kuyenela kukhala kosangalatsa kwa aliyense.

4. Kodi makolo angaganizile zinthu ziti pokonzekela kulambila kwa pabanja?

4 Makolo ganizilani zimene mungaphunzitse ana anu: Ngati muli ndi ana aang’ono, ganizilani mbali zotsatilazi:

• Konzani seŵelo mogwilitsila nchito nkhani ina ya m’Baibo. Uzani mwana wanu kuti avale ndi kucita zinthu mofanana ndi munthu wina wa m’Baibo, ndipo funsani ngati ena angam’zindikile.

• Lembani zithunzi-thunzi zopezeka m’zofalitsa zathu. Kumbukilani kuti: Zithunzi-thunzi zilibe mau, conco mungagwilitsile nchito zithunzi-thunzi zopezeka pa masamba a Galamukani! ya Cizungu zofunika kupakamo mitundu yake. Ndiyeno ziikeni pa malo oonekela m’nyumba mwanu.

• Citani zinthu zimene zingathandize ana anu kuganizilapo kwambili pa zimene amaphunzila. Afunseni kuti afotokoze mmene Nowa, Mose, Yosefe, Mariya, Petulo ndi ena anali kukhalila ndi mmene anali kuonela zinthu.

• Ŵelengelani pamodzi nkhani zimene mwasankha.

• Phunzilani kuimba Nyimbo za Ufumu. Kodi mungafune-fune cipangizo coimbila kapena kupanga kacipangizo koimbila nyimbo?

5. N’cifukwa ciani makolo ayenela kupempha Yehova kuti aŵathandize kuphunzitsa ana ao coonadi?

5 Makolo, Yehova amafuna kuti mukhale amai ndi atate ocita bwino. Conco mupempheni kuti akuthandizeni kuphunzitsa ana anu coonadi. (Ower. 13:8) Yehova angakuthandizeni kuphunzitsa ana anu kuti ‘akhale ndi nzelu zoŵathandiza kuti adzapulumuke kudzela m’cikhulupililo cokhudza Kristu Yesu.’—2 Tim. 3:15; Miy. 4:1-4.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani