Gwilitsilani Nchito Bwino Magazini Akale
Anthu sangapindule ndi magazini akale ngati tangowasunga cabe kapena kuwataya. Tiyenela kuyesetsa kuwagaŵila. Magazini imodzi ikhoza kudzutsa cidwi ca munthu ndi kum’cititsa kuti akonde coonadi. Ingamucititsenso kuti ayambe kuitanila pa dzina la Yehova. (Aroma 10:13, 14) Mfundo zotsatila zidzakuthandizani kugwilitsila nchito bwino magazini akale.
Polalikila m’magawo amene safoledwa kaŵili-kaŵili, ndi bwino kusiya magazini pobisika koma pamene mwininyumba angawaone.
Pamene ticita ulaliki wa poyela ku malo okwelela basi kapena sitima, funsani anthu ngati angafune zoŵelenga. Aonetseni makope osiyana-siyana a magazini athu akale kuti asankhepo.
Tikapita kucipatala, kapena kumalo ena m’gawo la mpingo wathu, ndi bwino kusiya magazini athu akale m’cipinda coyembekezela. Koma tisanacite zimenezo ndi bwino kupempha cilolezo kwa oyang’anila malowo ngati alipo. Ngati magazini athu alimo kale m’cipindaco, musaonjezelapo ena.
Pokonzekela maulendo obwelelako, coyamba ganizilani zimene munthu aliyense amene mufuna kukacezela amakonda. Kodi ali ndi banja? Kodi amakonda kuyenda maulendo? Kodi amakonda zolimalima? Kafufuzeni m’magazini akale ngati muli nkhani zimene angakonde kuŵelenga, ndiyeno kamuonetseni paulendo wanu wotsatila.
Munthu wacidwi akapezekanso panyumba pambuyo poyesa-yesa maulendo angapo, muonetseni magazini akale amene mwina sanalandile.