LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 11/14 tsa. 1
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuonetsa Anthu Cidwi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuonetsa Anthu Cidwi
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Kukonzekela Mau Athu Oyamba
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Mwininyumba Wokwiya
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Tizilemba Tikapeza Anthu Acidwi
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 11/14 tsa. 1

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuonetsa Anthu Cidwi

Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Yesu anali kuganizila munthu aliyense payekha ndipo anali kuonetsa cikondi anthuwo. Mwacitsanzo, pa cocitika cina iye anazindikila kuti munthu amene anali wogontha akanacita manyazi kumucilitsila pa gulu la anthu. Conco pomucilitsa, iye anatenga munthuyo n’kucoka naye pa khamu la anthu ndi kupita naye pambali. (Maliko 7:31-35) Yesu anaganizilanso ophunzila ake mwa kupewa kuwaphunzitsa zinthu zambili pa nthawi imodzi, podziŵa kuti sakanazimvetsa. (Yoh. 16:12) Yesu amaonetsabe anthu cidwi ngakhale pamene ali pa udindo wake kumwamba. (2 Tim. 4:17) Monga otsatila a Kristu, tifunika kutengela citsanzo cake. (1 Pet. 2:21; 1 Yoh. 3:16, 18) Kuonjezela apo, ulaliki wathu ungakhale wogwila mtima ngati tionetsa cidwi mwininyumba mwa kuyesetsa kudziŵa mmene zinthu zilili kwa iye, zimene amakonda ndiponso zimene zimamudetsa nkhawa. Iye akazindikila kuti tikucita zinthu momuganizila, angamvetsele zimene tikulankhula naye. Koma tikamacita ngati tabwela kudzamuuza cabe uthenga kapena kumusiila cofalitsa, munthuyo sangamvetsele.

Mmene Mungacitile:

  • Konzekelani bwino. Khalani omasuka, mwetulilani ndipo khalani aubwenzi.

  • Onani mmene zinthu zilili. Kodi mukuona zinthu zoonetsa kuti munthuyo ali ndi ana, amakonda zolimalima kapena ziweto? Kodi amakhulupilila zinthu zina zake za cipembedzo? Zikatelo, mungasinthe makambilano anu kuti agwilizane ndi mmene zinthu zilili kwa iye.

  • M’pempheni kuti anene maganizo ake, mvetselani mwachelu ndipo musam’dule mau. Muzimuyang’ana moonetsa kuti mukumvetsela. Ngati n’kotheka, muyamikileni kucokela pansi pa mtima. Pewani kutsutsana naye.

  • Muzisinthasintha ulaliki. Ngati n’kotheka sinthani ulaliki wanu kuti ukhale wogwilizana ndi nkhaŵa za munthuyo. Kucita zimenezi sikovuta, cifukwa tumapepala, mabulosha ndi magazini athu ali ndi nkhani zosiyanasiyana. Ngati mwafika pa nthawi imene munthuyo ali wotangwanika, zindikilani kuti mufunika kulankhula naye mwacidule.

Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:

  • Yesezani kucita izi pa nthawi ya kulambila kwa pabanja. Mungacite citsanzo ca mmene wofalitsa angasinthile ulaliki kuti ugwilizane ndi zimene mwininyumba wanena.

  • Pa misonkhano ina yokonzekela ulaliki wakumunda, m’bale amene akutsogolela angakambe njila za mmene tingaonetsele ena cidwi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani