LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp16 na. 4 tsa. 16
  • Kodi Baibulo Imakamba Ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibulo Imakamba Ciani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi anayambitsa cipembedzo ni anthu?
  • Kodi kukhala m’cipembedzo kuli ndi phindu?
  • Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Uthenga Wabwino Wonena za Cipembedzo ndi Uti?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
  • Mmene Zipembedzo Zonyenga Zimaimilako Mulungu Monama
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
wp16 na. 4 tsa. 16
Banja liyang’ana machalichi osiyanasiyana

Kodi Baibulo Imakamba Ciani?

Kodi anayambitsa cipembedzo ni anthu?

ANTHU ENA AMAKHULUPILILA kuti cipembedzo ni nkhani cabe ya anthu. Koma ena amaganiza kuti Mulungu amaseŵenzetsa cipembedzo kuti athandize anthu kukhala naye pa ubwenzi. Nanga inu muganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

Pali “kupembedza koyela ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu.” (Yakobo 1:27) Mulungu ni amene anayambitsa kulambila koyela kapena kuti koona.

ZINTHU ZINA ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

  • Mulungu amakondwela ndi cipembedzo cimene cimatsatila mfundo zoona za m’Baibulo.—Yohane 4:23, 24.

  • Zipembedzo zimene zimatsatila maganizo a anthu n’zopanda phindu.—Maliko 7:7, 8.

Kodi kukhala m’cipembedzo kuli ndi phindu?

MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Inde

  • Iyai

  • Nthawi zina

ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

“Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.” (Aheberi 10:24, 25) Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambila azisonkhana monga gulu.

ZINTHU ZINA ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

  • Amene amalambila Mulungu afunika kukhulupilila zinthu zofanana.—1 Akorinto 1:10, 11.

  • Amene ali m’cipembedzo ca zoona amakhala okondana ndi ogwilizana monga gulu la abale la padziko lonse.—1 Petulo 2:17

Nditumizileni buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse

Kuti mudziwe zambili, onani nkhani 5 m’buku ili, Zimene Baibulo Ingatiphunzitse lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti ya www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani