CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 120-134
“Thandizo Langa Licokela kwa Yehova”
Masalimo 120 mpaka 134 amadziŵika kuti ndi nyimbo zokwelela kumzinda. Ambili amakhulupilila kuti nyimbozi zinali kuimbidwa mwacisangalalo ndi Aisraeli popita ku Yerusalemu kukacita zikondwelelo zapacaka. Mzinda wa Yerusalemu unali pa malo okwela ku mapili a Yuda.
Citetezo ca Yehova cafotokozedwa kuti cili ngati. . .
121:3-8
mbusa wogalamuka
mthunzi woteteza ku dzuwa
msilikali wokhulupilika