September 12-18
MASALIMO 120-134
Nyimbo 33 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Thandizo Langa Licokela kwa Yehova”: (Mph. 10)
Sal. 121:1, 2—Popeza Yehova analenga zinthu zonse, tili ndi cifukwa comveka com’khulupilila (w04 12/15-CN, tsa. 12 ndime 3)
Sal. 121:3, 4—Yehova amakhala chelu nthawi zonse kuti aone zimene atumiki ake akufunikila (w04 12/15-CN, tsa. 12 ndime 4)
Sal. 121:5-8—Yehova ndi Mtetezi wokhulupilika wa anthu ake (w04 12/15-CN, tsa. 13 ndime 5-7)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Sal. 123:2—Kodi fanizo la “maso a atumiki” lili na mfundo yabwanji? (w06 9/1-CN, tsa. 15 ndime 4)
Sal. 133:1-3—Ni phunzilo liti limene tingatengepo pa salimo imeneyi? (w06 9/1-CN, tsa. 16 ndime 3)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Sal.127:1–129:8
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) wp16. Na. 5 nkhani ya pacikuto—Kuyankha mwininyumba amene ni wokwiya.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) wp16. Na. 5 nkhani ya pacikuto—Itanilani mwininyumba kumisonkhano.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) fg phunzilo 8 ndime 6—Thandizani wophunzila kuti aziseŵenzetsa mfundo zimene waphunzila.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Yehova Wanicitila Zambili: (Mph. 15) Tambitsani vidiyo ya pa jw.org. Yehova Wanicitila Zambili. (Pitani pa ZOKHUDZA IFE > ZIMENE TIMACITA.) Kambilanani mafunso otsatilawa: Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Crystal? Nanga zimenezi zinam’limbikitsa bwanji? N’ciani cimene anali kucita akayamba kudziona kuti ni wosafunika? Kodi nkhani ya Crystal yakuthandizani bwanji?
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia Mawu Omaliza ndime 1-13
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 119 na Pemphelo