CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YEREMIYA 44-48
Leka ‘Kufuna-funa Zinthu Zazikulu’
45:2-5
Baruki ayenela kuti anali nduna yophunzila bwino ya m’nyumba ya mfumu. Olo kuti anali kulambila Yehova ndi kuthandiza Yeremiya mokhulupilika, panthawi ina yake anacenjenekwa ndi zinthu zina. Iye anayamba kufuna-funa zinthu zazikulu,’ mwina kufuna udindo wokwelelapo m’bwalo la mfumu, kapena cuma. Anafunikila kusintha kalingalilidwe kake kuti apulumuke ciwonongeko ca Yerusalemu cimene cinali kubwela.