UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mumawakonda Kwambili Mawu a Mulungu?
M’Baibo muli mawu na maganizo a Yehova Mulungu, Mlembi wa buku lopatulika limeneli. (2 Pet. 1:20, 21) Mwa kugogomeza nkhani ya kukweza ulamulilo wa Mulungu kupitila mu Ufumu wake, Baibo imapatsa anthu ciyembekezo cakuti posacedwa, umoyo udzakhala wabwino. Baibo imaonetsanso umunthu wacikondi wa Atate wathu, Yehova.—Sal. 86:15.
Tonsefe timalemekeza Mawu a Yehova pa zifukwa zosiyana-siyana. Koma kodi timaonetsa kuti timakonda mphatso ya mtengo wapatali imeneyi mwa kuiŵelenga nthawi zonse, na kuseŵenzetsa mfundo zake mu umoyo wathu? Tiyeni tizionetsa mwa zocita zathu kuti tili na maganizo ofanana na a wamasalimo amene anati: “Ndimakonda kwambili cilamulo canu!—Sal. 119:97.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI, ANAILEMEKEZA KWAMBILI BAIBO—KAMBALI KAKE (WILLIAM TYNDALE), NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
N’cifukwa ciani William Tyndale anamasulila mbali zina za Baibo?
N’cifukwa ciani khama lake pomasulila Baibo linali locititsa cidwi?
Kodi makope a Baibo imene Tyndale anamasulila anali kuwazembetsa bwanji kuloŵa m’dziko la England?
Kodi aliyense wa ife angaonetse bwanji kuti amakonda Mawu a Mulungu