CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 32-33
Kodi Mukulimbikila kuti Mupeze Madalitso?
32:24-28
Kuti tilandile dalitso la Yehova, tifunika kulimbikila kuika zinthu za Ufumu patsogolo mu umoyo wathu. (1 Akor. 9:26, 27) Pamene titumikila Yehova, tiyenela kukhala na mzimu umene Yakobo anaonetsa polimbana na mngelo. Tingaonetse kuti tifuna dalitso la Yehova mwa . . .
Kukonzekela bwino misonkhano ya mpingo
Kutengako mbali nthawi zonse mu ulaliki
Kuyesetsa kuthandiza ena mumpingo
Olo kuti zinthu n’zovuta mu umoyo wanu, osaleka kupemphela kwa Yehova kuti akuthandizeni. Komanso, limbikilani pom’tumikila ndipo adzakudalitsani.
Dzifunseni kuti: ‘Mu umoyo wanga, ni mbali ziti zimene nifunika kulimbikilapo kuti nilandile dalitso la Yehova?’