LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • th phunzilo 12 tsa. 15
  • Mzimu Waubwenzi na Cifundo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mzimu Waubwenzi na Cifundo
  • Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Nkhani Zofanana
  • Kukamba Mwaumoyo
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Yesetsani Kuwafika pa Mtima Omvela
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Kukambilana Mwacibadwa
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Khalani Wolimbikitsa Komanso Wotsitsimula
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
Onaninso Zina
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
th phunzilo 12 tsa. 15

PHUNZILO 12

Mzimu Waubwenzi na Cifundo

Lemba losagwila mawu

1 Atesalonika 2:7, 8

ZOFUNIKILA: Lankhulani na mzimu woyenelela, ndipo onetsani kuti mumawaganizila omvela anu.

MOCITILA:

  • Ganizilani za omvela anu. Konzekeletsani mtima wanu poganizila mavuto amene omvela anu angamakumane nawo. Yesani kuganizila za mmene amamvelela.

  • Sankhani mawu mosamala. Yesetsani kutsitsimula omvela anu, kuwatonthoza, na kuwalimbikitsa. Pewani mawu amene angawakhumudwitse. Komanso pewani kukamba mawu onyoza omvela anu amene si Mboni, kapena kusuliza zikhulupililo zawo, zimene eni ake amazilemekeza.

  • Aikileni mtima omvela anu. Pokamba na mawu acifundo komanso magesca oyenelela, onetsani omvela anu kuti mumasamaladi za iwo. Samalaninso na nkhope yanu, muzimwetulila kaŵili-kaŵili.

    Tumalangizo tothandizila

    Osangodzipanga poonetsa mzimu waubwenzi kapena wacifundo. Ndipo poŵelenga, onetsani mzimu wa mbali imene mukuŵelenga, komabe osacita mopambanitsa kuti azitamanda imwe. Pokamba, mawu anu azimveka aubwenzi, olimbikitsa, komanso otsitsimula.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani