LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsa. 7
  • Misonkhano Ikulu-ikulu Yapacaka Imatipatsa Mwayi Woonetsana Cikondi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Misonkhano Ikulu-ikulu Yapacaka Imatipatsa Mwayi Woonetsana Cikondi
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Adziŵa zimene Tifunikila
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 January tsa. 7

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Misonkhano Ikulu-ikulu Yapacaka Imatipatsa Mwayi Woonetsana Cikondi

Mboni zocokela ku maiko ena za cikhalidwe cosiyana, zaima pamodzi kuti zijambulitse cithunzi pa msonkhano wa maiko.

N’cifukwa ciani misonkhano yathu ikulu-ikulu yapacaka imatisangalatsa kwambili? Monga mmene zinalili m’nthawi ya Aisiraeli, misonkhano ikulu-ikulu masiku ano imatipatsa mwayi wolambila Yehova pamodzi na okhulupilila anzathu mahandiledi, ngakhale masauzande kumene. Timakondwela na phwando la cakudya cauzimu conona. Timasangalalanso na mwayi wamtengo wapatali woyanjana na mabwenzi komanso mabanja athu. Timayamikila kwambili misonkhano imeneyi, cakuti timayesetsa kupezekapo masiku onse atatu.

Tikakhala na mwayi wosonkhana pamodzi, sitiyenela kungoganizila za mmene ife tingapindulile, koma tiyenela kuganizilanso za mmene tingaonetsele cikondi kwa ena. (Agal. 6:10; Aheb. 10:24, 25) Ngati titsegulila m’bale kapena mlongo wathu citseko kapena kusungila malo anthu okhawo amene tili nawo limodzi, timaonetsa kuti timaganizila zofuna za ena. (Afil. 2:3, 4) Misonkhano ikulu-ikulu imatipatsa mwayi wopanga mabwenzi atsopano. Pulogilamu isanayambe kapena ikatha, komanso pa nthawi yopumula, tingakhale na colinga codziŵana na winawake amene sitim’dziŵa. (2 Akor. 6:13) Ubwenzi umene tingapange pa zocitika zaconco, ungakhale mpaka kale-kale. Koposa zonse, anthu ena akaona cikondi ceni-ceni cimene timaonetsana, angasankhe kuyamba kutumikila nafe Yehova pamodzi.—Yoh. 13:35.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI MSONKHANO WA MAIKO WAKUTI “CIKONDI SICITHA”! NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti, ‘Msonkhano wa Maiko Wakuti ‘Cikondi Sicitha’!’ Mboni za m’dzikolo na zocokela ku maiko ena zikukumbatilana polandilana pa msonkhano wa maiko.

    Kodi abale na alongo ocokela ku maiko ena anaonetsedwa bwanji cikondi pa misonkhano ya maiko ya mu 2019?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti, ‘Msonkhano wa Maiko Wakuti ‘Cikondi Sicitha’!’ Abale na alongo a m’dziko limene munacitikila msonkhano wa maiko aima pamodzi kuti ajambulitse cithunzi.

    N’cifukwa ciani mgwilizano na cikondi zimene zili pakati pa anthu a Yehova n’zocititsa cidwi?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti, ‘Msonkhano wa Maiko Wakuti ‘Cikondi Sicitha’!’ Kagulu ka abale na alongo a ku Korea kanyamula cikwangwani cokhala na mawu olandila alendo obwela pa msonkhano, ndipo anyamula manja poonetsa kuti awalandila.

    Kodi abale a m’Bungwe Lolamulila anafotokoza mbali ziti za cikondi cacikhristu?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti, ‘Msonkhano wa Maiko Wakuti ‘Cikondi Sicitha’!’ Kamtsikana kanyamula ‘Baibo ya Dziko Latsopano’ imene kangolandila kumene, ndipo kali na cimwemwe.

    Kodi mungacite ciani kuti muthandizile kuonetsa cikondi pa misonkhano yathu ikulu-ikulu?

    Kodi cikondi cacikhristu cinawagwilizanitsa bwanji abale athu ku Germany na ku South Korea?

  • Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani