LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsa. 9
  • Tidzapeza Ufulu M’tsogolo mwa Thandizo la Mulungu na Khristu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tidzapeza Ufulu M’tsogolo mwa Thandizo la Mulungu na Khristu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Amatithandiza Kupilila Mayeso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Mmene Tingakhalilebe Acimwemwe Popilila Mayeso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Yamikani Yehova Ndipo Mudzadalitsidwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 January tsa. 9
Yesu akuyang’ana padziko lapansi atakhala pampando wacifumu kumwamba, ndipo kumbuyo kwake kuli mpando wacifumu wa Yehova wowala.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Tidzapeza Ufulu M’tsogolo mwa Thandizo la Mulungu na Khristu

Kodi ni mavuto ati amene mumakumana nawo tsiku na tsiku? Kodi ndimwe mutu wa banja ndipo mukuvutika kusamalila maudindo ambili-mbili? Kodi ndimwe kholo limene likulela lokha ana ndipo mukuvutika kuwasamalila? Kodi ndimwe wacicepele amene mumavutitsidwa na anzanu kusukulu? Kodi mukuvutika cifukwa ca matenda kapena mavuto obwela cifukwa ca ukalamba? Tonsefe tikukumana na mavuto enaake. Akhristu ena akukumana na mavuto ambili panthawi imodzi. Koma tidziŵa kuti posacedwa, tidzamasulidwa ku mavuto amenewa.—2 Akor. 4:16-18.

Pamene tiyembekezela nthawi imeneyo, timapeza citonthozo podziŵa kuti Yehova amamvetsetsa mavuto athu, amayamikila kukhulupilika na kupilila kwathu, ndipo watisungila madalitso osaneneka kutsogolo. (Yer. 29:11, 12) Yesu nayenso amatidela nkhawa. Pamene tigwila nchito zathu zacikhristu, iye anatilonjeza kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu.” (Mat. 28:20) Pamene tipatula nthawi yosinkha-sinkha za ufulu umene tidzakhala nawo mu Ufumu wa Mulungu, timalimbitsa ciyembekezo cathu, ndipo timakhala otsimikiza mtima kupilila mayeselo amene tikumana nawo.—Aroma 8:19-21.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI PAMENE MPHEPO YA MKUNTHO IKUYANDIKILA, PITILIZANI KUYANG’ANITSITSA YESU!—MADALITSO A UFUMU A MTSOGOLO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Cinacitika n’ciani kuti mtundu wa anthu ukhale wotalikilana na Mulungu? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

  • Kodi anthu okhulupilika kwa Yehova ayembekezela madalitso otani?

  • Kodi madalitso am’tsogolo amenewa adzatheka bwanji?

  • Ni madalitso ati a m’dziko latsopano amene mukuyembekezela mwacidwi?

Zithunzi: Anthu akusangalala na madalitso m’Paradaiso. 1. Mlongo akukumbatila munthu amene waukitsidwa. 2. Akusangalala na cakudya cokwanila, dziko lapansi la ukhondo, na mtendele.

Yelekezelani kuti muli m’dziko latsopano

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani