Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
JANUARY 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 18-19
“Khalanibe na Khalidwe Loyela”
Mmene Tingadzitetezele ku Msampha wa Satana
Pambuyo pofotokoza zonyansa zimene anthu a mitundu ina anali kucita, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Musakacite zimene amacita m’dziko la Kanani, kumene ndikukulowetsani. . . . Dzikolo n’lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga cifukwa ca kulakwa kwake.” Kwa Mulungu woyela wa Aisiraeli, makhalidwe a Akanani anali onyansa kwambili, cakuti zinacititsa dziko lawo kukhala lodetsedwa.—Lev. 18:3, 25.
Yehova Amatsogolela Anthu Ake
13Mafumu okhulupilika amenewo anali osiyana kwambili ndi atsogoleli a mitundu ina amene anali kutsogoleledwa ndi nzelu za anthu zosathandiza konse. Mwacitsanzo, pansi pa utsogoleli wacikanani, anthu anali kucita zinthu zonyansa, monga kugonana pa cibululu, kugonana amuna kapena akazi okha-okha, kugona nyama, kupeleka nsembe ana, ndi kulambila mafano. (Lev. 18:6, 21-25) Kuwonjezela apo, atsogoleli acibabulo ndi aciiguputo sanali kutsatila malamulo a zaukhondo ogwilizana ndi sayansi amene Mulungu anapatsa Aisiraeli. (Num. 19:13) Mosiyanako, anthu a Mulungu akale anaona mmene atsogoleli awo okhulupilika analimbitsila ciyelo cauzimu, cakuthupi ndi makhalidwe abwino. N’zoonekelatu kuti Yehova anali kuwatsogolela.
Zimene Mulungu Adzacita Pothetsa Zinthu Zoipa
Nanga bwanji za aja amene mwadala amakana kusintha njila zawo ndipo amangopitilizabe kucita zinthu zoipa? Ganizilani lonjezo ili losapita m’mbali lakuti: “Oongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda colakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzacotsedwa padziko lapansi ndipo acinyengo adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) Anthu oipa sadzakhalaponso kuti acite zoipa. M’dziko lamtendele limenelo, anthu omvela adzamasuka pang’onopang’ono ku ucimo.—Aroma 6:17, 18; 8:21.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w06 6/15 22 ¶11
“Ha! Ndikondadi Cilamulo Canu”
11Mbali yaciŵili ya Cilamulo ca Mose imene inasonyeza kuti Mulungu amadela nkhawa anthu ake inali yonena za ufulu wokunkha. Yehova analamula kuti mlimi wa mu Isiraeli akakolola mbewu za m’munda mwake, anthu osauka aziloledwa kukunkha zinthu zimene anchito okolola asiya. Alimi sanali kuloledwa kukolola m’mphepete monse mwa minda yawo, ndipo sanali kuloledwa kukolola mphesa zotsalila m’munda kapena maolivi otsalila. Mitolo ya zokolola yomwe yaiŵalidwa m’munda sinayenela kudzatengedwa. Amenewa anali malamulo acikondi othandiza anthu osauka, alendo, ana amasiye, ndi akazi amasiye. N’zoona kuti anthuwa anafunika kugwila nchito mwakhama kuti athe kukunkha, koma cifukwa ca malamulo amenewa, akanapewa kupemphapempha.—Levitiko 19:9, 10; Deuteronomo 24:19-22; Salimo 37:25.
JANUARY 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 20-21
“Yehova amapatula anthu ake”
w04 10/15 11 ¶12
Kodi Muli ndi Cifukwa Comveka Coyembekezela Paradaiso?
12Komabe pali cinthu cina cimene sitiyenela kucinyalanyaza. Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “Muzisunga malamulo onse amene ndikukupatsani lelo, kuti mukhale amphamvu ndi kuti mulowedi m’dziko limene mukuwolokelako ndi kulitenga kukhala lanu.” (Deuteronomo 11:8) Dziko limeneli linachulidwanso pa Levitiko 20:22, 24. Lembali limati: “Inu muzisunga malangizo anga onse ndi zigamulo zanga zonse, kuti dziko limene ndikukulowetsani kuti mukhalemo lisakusanzeni. N’cifukwa cake ndinakuuzani kuti: ‘Inuyo mudzatenga dzikolo ndipo ine ndidzalipeleka m’manja mwanu kuti likhale lanu, dziko loyenda mkaka ndi uci. Inde, kuti alandile Dziko Lolonjezedwa panafunika kuti Aisiraeli akhale paunansi wabwino ndi Yehova Mulungu. Mulungu analola Ababulo kumenyana ndi Aisiraeli na kuwacotsa m’dziko lawo cifukwa cakuti sanamumvele.
it-1 1199
Colowa
Colowa ni katundu aliyense wa munthu womwalila amene amapelekedwa kwa woyenela kulandila katunduyo kapena womuloŵa m’malo. Ni ciliconse cimene munthu amalandila kucokela kwa makolo ake kapena kwa munthu amene iye wamuloŵa m’malo. Mneni waciheberi amene kaŵili-kaŵili amamasulidwa kuti coloŵa ni na·chalʹ (dzina, na·chalahʹ). Mawuwa amatanthauza kulandila kapena kupeleka colowa, kaŵili-kaŵili cifukwa cakuti anthu aloŵana m’malo. (Num. 26:55; Ezek. 46:18) Liwu lakuti ya·rashʹ, nthawi zina amaliseŵenzetsa m’lingalilo la “kuloŵa m’malo monga wolandila colowa.” Koma nthawi zambili limatanthauza “kutenga cinthu kukhala cako,” popanda kupeleka lingalilo la kuloŵa m’malo munthu. (Gen. 15:3; Lev. 20:24) Nthawi zina, limatanthauzanso “kulanda malo” kapena “kupitikitsa” mwa kucita nkhondo. (Deut. 2:12; 31:3) Mawu acigiriki omasulidwa kuti colowa anacokela ku liwu lakuti kleʹros, amene poyamba anali kutanthauza “mayele” koma m’kupita kwa nthawi anayamba kutanthauza gawo, ndipo pamapeto pake anayamba kutanthauza “colowa.”—Mat. 27:35; Mac. 1:17; 26:18.
it-1 317 ¶2
Mbalame
Pambuyo pa Cigumula, Nowa anapeleka zina mwa “zouluka zoyela” pamodzi na nyama monga nsembe. (Gen. 8:18-20) Pambuyo pake, Mulungu analola anthu kudya mbalame malinga ngati sanadye magazi ake. (Gen. 9:1-4; yelekezelani na Lev. 7:26; 17:13.) Conco, cioneka kuti mbalame zina zinali kuonedwa ‘zoyela’ cifukwa cakuti Mulungu analola kuti zizipelekedwa nsembe. Baibo imaonetsa kuti Cilamulo ca Mose cikalibe kukhazikitsidwa, panalibe mbalame imene inali kuonedwa kuti ni “yodetsedwa” yoti munthu sangadye. (Lev. 11:13-19, 46, 47; 20:25; Deut. 14:11-20) Malemba safotokoza mwacindunji zifukwa zimene zinali kupangitsa mbalame zina kukhala “zodetsedwa.” Conco, ngakhale kuti mbalame zambili zimene zinali kuonedwa zodetsedwa ni zija zimene zimadya nyama zinzake, si zonse zodya nyama zinzake zimene zinali zodetsedwa. Lamulo loletsa kudya nyama zina linathetsedwa pamene pangano latsopano linakhazikitsidwa. Ndipo Mulungu anaonetsa bwino zimenezi kupitila m’masomphenya amene Petulo anaona.—Mac. 10:9-15.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 563
Kudziceka-ceka
Cilamulo ca Mulungu cinali kuletsa mwacindunji mcitidwe wa kudziceka-ceka pathupi cifukwa ca akufa. (Lev. 19:28; 21:5; Deut. 14:1) Mcitidwe umenewu unali woletsedwa cifukwa Aisiraeli anali anthu oyela kwa Yehova, cuma cake capadela. (Deut. 14:2) Pokhala mtundu woyela, Aisiraeli anafunika kupewa kulambila mafano kwa mtundu ulionse. Komanso, kuonetsa cisoni mwa kucita kudziceka-ceka pathupi, kunali kosayenela ngakhale pang’ono kwa anthu amene anali kudziŵa bwino mkhalidwe wa anthu akufa, ndiponso amene anali na ciyembekezo cakuti akufa adzauka. (Dan. 12:13; Aheb. 11:19) Cina, lamulo loletsa kudziceka-ceka likanathandiza Aisiraeli kuona kufunika kolemekeza matupi awo monga mbali ya cilengedwe ca Mulungu.
JANUARY 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 22-23
“Zikondwelelo za Pacaka Zokhala na Tanthauzo kwa Ife”
it-1 826-827
Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Cofufumitsa
Tsiku loyamba la Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Cofufumitsa, linali tsiku la msonkhano wopatulika komanso sabata. Patsiku laciŵili, pa Nisani 16, Aisiraeli anali kupeleka mtolo wa zipatso zoyambilila kuca za balele kwa wansembe. Iyi inali mbewu yoyambilila kuca ku Palesitina. Ngati Aisiraeli akalibe kucita cikondweleloci, sanali kuloledwa kudya mbewu zatsopano, mkate, kapena mbewu zokazinga zoyambilila kuca. Mophiphilitsila, wansembe anali kupeleka zipatso zoyambilila kucazo kwa Yehova mwa kuweyulila mtolo wa mbewuzo uku na uku. Pa nthawiyi, mwana wa nkhosa wosapitilila caka cimodzi, anali kupelekedwa monga nsembe yopseleza pamodzi na nsembe yambewu yothila mafuta komanso nsembe yacakumwa. (Lev. 23:6-14) Panalibe lamulo lakuti mbewu kapena ufa, zizitenthedwa paguwa lansembe monga mmene ansembe anali kucitila pambuyo pake. Kuwonjezela pa nsembe ya zipatso zoyambilila kuca yoimila gulu kapena mtundu wonse wa Aisiraeli, banja lililonse na munthu aliyense amene anali na malo mu Isiraeli, anapatsidwa mwayi wopeleka nsembe zaciyamiko pa cikondweleloci.—Eks. 23:19; Deut. 26:1, 2.
Kufunika Kwake. Malinga na Ekisodo 12:14-20, kudya mikate yopanda cofufumitsa panthawiyi, kunali kogwilizana na malangizo amene Mose analandila kucokela kwa Yehova. Malangizowo, anaphatikizapo lamulo lamphamvu limene lili pa vesi 19 lakuti: “Musamadzapezeke mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi cofufumitsa m’nyumba zanu kwa masiku 7.” Pa Deuteronomo 16:3 mikate yopanda cofufumitsa imachedwanso kuti “mkate wa nsautso.” Mikateyo inali kukumbutsa Ayuda caka na caka zakuti anacoka cothamanga m’dziko la Iguputo (moti analibe nthawi yoika zofufumitsa ku ufa wawo wokanda [Eks. 12:34]). Izi zinali kukumbutsa Aisiraeli za nsautso na ukapolo umene iwo analimo asanawomboledwe, monga mmene Yehova anawauzila kuti ‘muzikumbukila tsiku limene munatuluka m’dziko la Iguputo masiku onse a moyo wanu.’ Cikondwelelo ca mikate yopanda cofufumitsa, cinali kukumbutsa Aisiraeli kuti tsopano ali pa ufulu monga mtundu, komanso kuti Yehova ndiye Mpulumutsi wawo. Kukumbukila zimenezi, kunayala maziko abwino acikondwelelo coyamba pa zikondwelelo zitatu zikulu-zikulu za pacaka zimene iwo anali kucita.—Deut. 16:16.
it-2 598 ¶2
Pentekosite
Zipatso zoyambilila kuca za tiligu, zinali kupelekedwa mosiyana na zipatso zoyambilila kuca za balele. Magawo aŵili mwa magawo 10 a muyezo wa efa (malita 4.4; makwati 4) a ufa wosalala wa tiligu pamodzi na zofufumitsa anali kuziphika n’kupanga mitanda iŵili ya mkate. Mitandayo inafunika kukhala yocokela m’nyumba zawo. Izi zinatanthauza kuti inafunika kukhala yofanana na mitanda ya mkate imene iwo anali kudya panyumba zawo tsiku na tsiku, osati yoseŵenzetsa pa zocitika zopatulika. (Lev. 23:17) Nsembe zopseleza komanso nsembe yamacimo, anali kuzipelekela pamodzi na mitanda ya mkate imeneyi, ndipo ana a nkhosa aŵili amphongo anali kuwapeleka monga nsembe yaciyanjano. Wansembe anali kuweyula mitanda ya mkateyo ndi ana a nkhosawo pamaso pa Yehova, mwa kuika manja ake pansi pa mitandayo komanso panthuli za nyama ya ana a nkhosa n’kumaziyendetsa uku ndi uku, kuonetsa kuti akuzipeleka kwa Yehova. Pambuyo pakuti mitanda ya mkateyo na ana a nkhosawo zapelekedwa kwa Yehova, zinthuzo zinali kukhala za wansembe kuti azidye monga nsembe yaciyanjano.—Lev. 23:18-20.
Kodi Mumayendela Limodzi ndi Gulu la Yehova?
11Gulu la Yehova limatilimbikitsa kutsatila malangizo a Paulo akuti: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena acizolowezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tionjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” (Aheb. 10:24, 25) Zikondwelelo za pacaka ndi misonkhano ina zinalimbitsa Aisiraeli mwa kuuzimu. Zocitika zina monga Cikondwelelo ca Misasa m’masiku a Nehemiya zinali nthawi yosangalatsa. (Eks. 23:15; Neh. 8:9-18) Mofananamo, ifenso timapindula ndi misonkhano yampingo, yadela ndi yacigawo. Tiyeni tiziyesetsa kupezeka pamisonkhano yonse imeneyi kuti tikhale acimwemwe ndi olimba kuuzimu.—Tito 2:2.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Khalanibe na Mtima Wamphumphu!
3Kwa atumiki a Mulungu, kukhala na mtima wamphumphu kumatanthauza kukonda Yehova na mtima wonse, komanso kudzipeleka kwathunthu kwa iye, moti pa zosankha zawo zonse, amaika Mulungu patsogolo. Tiyeni tione mmene mawuwa akuwaseŵenzetsela m’Baibo. M’Baibo, mawu akuti, “mtima wamphumphu,” kweni-kweni amatanthauza cinthu cathunthu, cabwino-bwino, kapena conse. Mwacitsanzo, Aisiraeli anali kupeleka nsembe za nyama kwa Yehova. Ndipo Cilamulo cinakamba kuti nyamazo zinafunika kukhala zopanda cilema. (Lev. 22: 21, 22) Aisiraeli sanaloledwe kupeleka nsembe nyama zodwala, zopanda mwendo umodzi, khutu, kapena diso. Yehova anali kufuna kuti nyama yopelekedwa nsembe izikhala yathunthu, komanso yabwino-bwino. (Mal. 1:6-9) Izi zionetsa kuti Yehova amafuna kuti tikhale na mtima wamphumphu kapena kuti wathunthu. Tiyelekezele motele: Tikapita ku msika, sitingagule cipatso conyemeka, buku long’ambika mapeji, kapena cipangizo cowonongeka mbali zina. Timafuna kugula cinthu cimene n’cathunthu, komanso cabwino-bwino. Yehova naye amafuna kuti tikhale okhulupilika kwathunthu kwa iye. Amafunanso kuti tizim’konda na mtima wonse.
JANUARY 25-31
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 24-25
“Caka ca Ufulu Komanso Ufulu wa M’tsogolo”
it-1 871
Ufulu
Mulungu wa Ufulu. Yehova ni Mulungu wa ufulu. Anamasula mtundu wa Isiraeli mu ukapolo ku Iguputo. Iye anawauza kuti malinga ngati adzamvela malamulo ake, sadzasoŵa ciliconse. (Deut. 15:4, 5) Davide anakamba kuti anthu okhala mu nsanja za Yerusalemu adzakhala “opanda nkhawa iliyonse.” (Sal. 122:6, 7) Komabe, Cilamulo cinapeleka mwayi wakuti ngati munthu wakhala wosauka angadzigulitse n’kukhala kapolo n’colinga cakuti azipeza zosoŵa za banja lake komanso za iye mwini. Koma Cilamulo cinapelekanso mwayi wakuti kapolo waciheberi akatumikila kwa zaka 6, m’caka ca 7 azimasulidwa. (Eks. 21:2) M’Caka ca Ufulu, cimene cinali caka ca 50 ciliconse, ufulu unali kulengezedwa kwa onse okhala m’dziko la Isiraeli. Kapolo aliyense waciheberi anali kumasulidwa, ndipo munthu aliyense anali kubwelela kumalo ake.—Lev. 25:10-19.
it-1 1200 ¶2
Colowa
Popeza kuti malo anali colowa ca banja ku mibadwo-mibadwo, zinali zosatheka kuwagulitsa mpaka kale-kale. Kugulitsa malo, kunali monga kucititsa lendi cabe potengela phindu la zokolola za pamalopo. Mtengo wa malowo, unali kudalila pa kuculuka kwa zaka zimene zatsala kuti afike m’Caka ca Ufulu. M’Caka ca Ufulu, malo onse anali kubwezedwa kwa eniake, ngati eniakewo sanawawombole Caka ca Ufulu cisanafike. (Lev. 25:13, 15, 23, 24) Lamulo limeneli linaphatikizapo nyumba zokhala m’midzi yopanda linga, zimene zinali kuonedwa monga mbali ya munda wa kunja kwa mzinda. Nyumba ya mu mzinda wokhala ndi linga, mwini wake anali na ufulu woiwombola caka cimodzi cisanathe kucokela pamene anaigulitsa. Koma ngati sanaiwombole caka cimodzico cisanathe, nyumbayo inali kukhala ya wogulayo mpaka kale-kale. Ponena za nyumba zokhala m’mizinda ya Alevi, Aleviwo anali na ufulu wowombola nyumba zawo m’mizindamo mpaka kale-kale cifukwa analibe malo monga colowa cawo.—Lev. 25:29-34.
it-2 122-123
Caka ca Ufulu
Kumvela lamulo la Caka ca Ufulu kunathandiza mtundu wa Isiraeli kupewa vuto limene timaona m’maiko ambili masiku ano, lokhala na magulu aŵili a anthu, olemela kwambili ndiponso osauka kwambili. Makonzedwe amenewa anali kupindulitsa munthu aliyense payekha komanso mtundu wonse, cifukwa palibe aliyense amene akanakhala wosauka kwambili kapena wosathandiza pa citukuko ca dziko cifukwa ca mavuto a zacuma. Koma onse anali na mwayi woseŵenzetsa maluso na mphamvu zawo popititsa patsogolo citukuko ca dziko. Aisiraeli akakhala omvela, Yehova anali kudalitsa zokolola za m’minda yawo na kuwaphunzitsa, ndipo iwo anali kusangalala na boma langwilo komanso ulemelelo, zimene zimatheka kokha cifukwa colamulidwa na Mulungu.—Yes. 33:22.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w09 9/1 22 ¶4
Kodi Muyenela Kucita Ciani Mukakhumudwitsidwa?
Ngati munthu waciisiraeli wapweteka mnzake ndi kum’cotsa diso, m’Cilamulo munali cilango coyenela. Komabe, munthu amene wapwetekedwayo si amene anali kupeleka cilango kwa munthuyo kapena acibale ake. Cilamulo cinali kunena kuti munthuyo akatule nkhaniyo kwa anthu oyenelela omwe anali oweluza kuti akaweluze nkhaniyo. Kudziŵa lamulo lakuti munthu waciwawa kapena wolimbikitsa zaciwawa anayenela kulangidwa mofanana ndi mmene wapwetekela mnzakeyo, kunali kuthandiza kwambili kuti anthu asamabwezelane. Komanso pali zifukwa zina.
FEBRUARY 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 26-27
“Zimene Tingacite Kuti Tilandile Madalitso a Yehova”
w08 4/15 4 ¶8
Kanani Zinthu “Zopanda Pake”
8Kodi zingatheke bwanji “Cuma” kukhala mulungu? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tiganizile za mwala umene unali m’munda, m’nthawi ya Aisiraeli. Mwala umenewo akanatha kumangila nyumba kapena mpanda. Koma mwala umenewo akanati aupange “cipilala copatulika” kapena “mwala wokhala ndi zithunzi zojambula mocita kugoba,” ukanakhala copunthwitsa anthu a Yehova. (Lev. 26:1) Mofanana ndi zimenezi, ndalama zili na nchito yake. Timafunikila ndalama kuti tipeze zofunika pamoyo, ndipo tingazigwilitse nchito bwino potumikila Yehova. (Mlal. 7: 12; Luka 16:9) Koma mtima wathu ukakhala pa kufuna-funa ndalama m’malo moika patsogolo utumiki wathu wacikhristu, pamenepo ndalamazo zimakhala mulungu wathu. (Ŵelengani 1 Timoteyo 6:9, 10.) Popeza kuti anthu m’dzikoli amafuna kwambili kulemela, ifeyo tionetsetse kuti nkhani ya ndalamayi tikuiona bwino.—1 Tim. 6:17-19.
it-1 223 ¶3
Mantha
Cifukwa ca mmene Yehova anaseŵenzetsela Mose na mmene anacitila naye zinthu, Mose anacita zinthu zazikulu ndi zoopsa (m’Ciheberi, moh·raʼʹ) pamaso pa anthu a Mulungu. (Deut. 34:10, 12; Eks. 19:9) Aisiraeli amene anali na cikhulupililo anali kuopa ulamulilo wa Mose moyenelela. Iwo anali kudziŵa kuti Mulungu anali kukamba nawo kupitila mwa iye. Kuwonjezela apo, Aisiraeli anafunika kuopa malo opatulika a Yehova. (Lev. 19:30; 26:2) Izi zinatanthauza kuti Aisiraeli anafunika kuonetsa kuti anali kulemekeza malo opatulika a Yehova mwa kumulambila mmene iye anawalamulila, komanso mwa kukhala na makhalidwe ogwilizana na malamulo ake onse.
w91 3/1 17 ¶10
Lolani “Mtendele wa Mulungu” Ucinjilize Mtima Wanu
10Yehova anauza mtunduwo kuti: “Mukapitiliza kutsatila malangizo anga ndi kusunga malamulo anga, ndidzakugwetselani mvula pa nthawi yake. Nthaka idzakupatsani cakudya, ndipo mitengo ya m’munda idzakupatsani zipatso zake. Ndidzakupatsani mtendele m’dzikolo, moti mudzagona pansi popanda wokuopsani. M’dziko lanu simudzapezeka zilombo zoopsa zakuchile, ndipo simudzadutsa lupanga. Motelo ndidzayendadi pakati panu ndi kukusonyezani kuti ine ndine Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga.” (Levitiko 26:3, 4, 6, 12) Isiraeli akanatha kusangalala na mtendele cifukwa cakuti anali wotetezeka kwa adani ake, anali na cuma cakuthupi camwana alilenji, komanso unansi wathithithi na Yehova. Koma izi zikanadalila pa kumamatila kwake ku Cilamulo ca Yehova.—Salimo 119:165.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 617
Mlili
Wobwela Cifukwa Cosatsatila Cilamulo ca Mulungu. Mtundu wa Aisiraeli unacenjezedwa kuti ngati wakana kutsatila cipangano ca Mulungu, iye ‘adzawatumizila mlili pakati pawo.’ (Lev. 26:14-16, 23-25; Deut. 28:15, 21, 22) Baibo imagwilizanitsa thanzi labwino, kaya lakuthupi kapena lakuuzimu, na dalitso la Mulungu. (Deut. 7:12, 15; Sal. 103:1-3; Miy. 3:1, 2, 7, 8; 4:21, 22; Chiv. 21:1-4) Ndipo matenda imawagwilizanitsa na ucimo na kupanda ungwilo. (Eks. 15:26; Deut. 28:58-61; Yes. 53:4, 5; Mat. 9:2-6, 12; Yoh. 5:14) N’zoona kuti nthawi zina Yehova Mulungu anali kubweletsa matenda mwacindunji komanso pa nthawi yomweyo kwa anthu, monga khate la Miriamu, Uziya, ndiponso Gehazi. (Num. 12:10; 2 Mbiri 26:16-21; 2 Maf. 5:25-27) Koma zioneka kuti nthawi zambili matenda na milili zinali kubwela cifukwa ca zotsatilapo za makhalidwe oipa a anthu kapena mitundu. Iwo anakolola zimene anafesa; matupi awo anakanthidwa na matenda cifukwa ca zoipa zimene anacita. (Agal. 6:7, 8) Pokamba za anthu amene anali kucita khalidwe lonyansa la ciwelewele, mtumwi Paulo anati Mulungu “anawasiya kuti acite zonyansa kuti matupi awo acitidwe cipongwe . . . ndi kulandililatu mphoto yoyenelela kulakwa kwawo.”—Aroma 1:24-27.
FEBRUARY 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 1-2
“Yehova Alinganiza Anthu Ake Mwadongosolo”
w94 12/1 9 ¶4
Malo Oyenela a Kulambila Yehova M’miyoyo Yathu
4Mukanakhala m’mwamba ndi kuyang’ana Aisiraeli ogonela m’cipululu, kodi mukanaona ciani? Malo aakulu, koma adongosolo a mahema okhalamo pafupi-fupi anthu mamiliyoni atatu kapena kuposapo, osonkhanitsidwa m’magulu a mafuko atatu-atatu kumpoto, kum’mwela, kum’maŵa, ndi kumadzulo. Mukanayang’anitsitsa capafupi, mukanaonanso gulu lina pafupi na pakati pa msasa. M’tumagulu twa mahema tunayi tumenetu munali kukhala mabanja a fuko la Levi. Pakati peni-peni pa msasa, pamalo ocingidwa ndi mpanda wa nsalu, panali cimango capadela. Cimeneci cinali “cihema cokumanako,” kapena cihema, cimene Aisiraeli “aluso” anamanga malinga na pulani ya Yehova.—Numeri 1:52, 53; 2:3, 10, 17, 18, 25; Ekisodo 35:10.
it-1 397 ¶4
Msasa
Msasa wa Aisiraeli umenewu unali waukulu kwambili. Malinga na ziŵelengelo zili pamwambapa, amuna onse omenya nkhondo anakwana 603,550. Ndipo tikaphatikiza ciŵelengelo ca akazi ndi ana, okalamba ndi olemala, Alevi okwana 22,000 na “khamu la anthu a mitundu yosiyana-siyana,” n’kutheka kuti onse pamodzi analipo 3,000,000 kapena kuposelapo. (Eks. 12:38, 44; Num. 3:21-34, 39) Kukula kwa malo amene anthuwo anamangapo msasa sikudziŵika bwino-bwino. Maganizo a anthu ponena za kukula kwa malowo amasiyana-siyana kwambili. Koma Baibo imakamba kuti pamene anthuwo anamanga msasa moyang’anana na Yeriko m’cigwa ca Mowabu, msasawo unali “kuyambila ku Beti-yesimoti mpaka ku Abele-sitimu.”—Num. 33:49.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 764
Kulemba Anthu m’Kaundula
Kalembela amene nthawi zambili anali kucitika mwa kulemba maina a anthu na mizela yawo yobadwila, malinga na mafuko awo komanso mabanja awo. Kumeneku sikunali kungoŵelenga anthu n’colinga cofuna kudziŵa cabe ciŵelengelo cawo. M’nthawi za Baibo, kuŵelenga anthu kunali kucitika pa zifukwa zosiyana-siyana, monga zokhudza kukhometsa msonkho, kuloŵa usilikali, kapena (ponena za Alevi), kudziŵa amene angapatsidwe nchito pa malo opatulika.
FEBRUARY 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 3-4
“Utumiki wa Alevi”
it-2 683 ¶3
Ansembe
Pa nthawi ya Pangano la Cilamulo. Pamene Aisiraeli anali mu ukapolo ku Iguputo, Yehova anadzipatulila mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa wa Aisiraeli, panthawi imene anali kuwononga ana oyamba kubadwa a Aiguputo pa mlili wa namba 10. (Eks. 12:29; Num. 3:13) Ana oyamba kubadwa amenewa anali a Yehova kuti nchito yawo izikhala kum’citila utumiki wopatulika basi. Mulungu akanafuna, akanatenga ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli kuti akhale ansembe komanso ogwila nchito yosamalila pa malo opatulika. Koma mogwilizana na cifunilo cake, iye anatenga amuna a m’fuko la Levi kuti azicita utumiki umenewu. Pa cifukwa cimeneci, Mulungu analola mtundu wa Isiraeli kupeleka amuna a fuko la Levi m’malo mwa ana aamuna oyamba kubadwa a mafuko 12 enawo (mbadwa za ana a Yosefe, Efraimu na Manase, zinaŵelengedwa monga mafuko aŵili). Ataŵelenga, anapeza kuti ana aamuna oyamba kubadwa osakhala ana aamuna a fuko la Levi, oyambila mwezi umodzi kupita m’tsogolo anali 273 kuposa amuna a fuko la Levi. Conco Mulungu anafuna dipo la masekeli asanu (madola 11) pa mwana aliyense mwa ana 273 amenewo. Ndalamazo zinapelekedwa kwa Aroni ndi ana ake. (Num. 3:11-16, 40-51) Izi zisanacitike, Yehova anali atapatula kale amuna a m’banja la Aroni a fuko la Levi kuti akhale ansembe mu Isiraeli.—Num. 1:1; 3:6-10.
it-2 241
Alevi
Nchito zawo. Panali mabanja atatu a Alevi ocokela mwa ana a Levi awa: Gerisoni (Gerisomu), HS2Kohati, HS2ndi HS3Merari. (Gen. 46:11; 1 Mbiri 6:1, 16) Lililonse la mabanja amenewa linapatsidwa malo pafupi na cihema copatulika m’cipululu. Banja lacikohati la Aroni linali kumanga msasa kutsogolo kwa cihema copatulika, mbali ya kum’maŵa. Akohati enawo anali kumanga msasa wawo kum’mwela kwa cihema copatulika, Agerisoni kumadzulo, ndipo a Merari kumpoto. (Num. 3:23, 29, 35, 38) Nchito yomanga cihema copatulika, kucipasula, na kucinyamula inali ya Alevi. Nthawi yosamuka ikakwana, Aroni ndi ana ake ndiwo anali kucotsa nsalu yochinga, imene inali kupanga malile pakati pa Malo Oyela na Malo Oyela Koposa n’kuphimba nayo likasa la umboni, maguwa ansembe, ndiponso zipangizo zina zopatulika na ziwiya zake. Kenako Akohati anali kunyamula zinthu zimenezo. Agerisoni ndiwo anali kunyamula nsalu za cihema copatulika, nsalu zake zophimba, nsalu zochinga, nsalu za mpanda wa bwalo, komanso zigwe zolimbitsila mpandawo (mwacionekele zinali zigwe za cihemaco). Amerari anali kusamalila mafelemu a cihema copatulika, mizati yake, zitsulo zokhazikapo mafelemu na mizati, zikhomo na zigwe zake (zigwe zolimbitsila mpanda wozungulila cihema copatulika).—Num. 1:50, 51; 3:25, 26, 30, 31, 36, 37; 4:4-33; 7:5-9.
it-2 241
Alevi
M’nthawi ya Mose, Mlevi akakwanitsa zaka 30 m’pamene anali kugwila nchito zonse zaulevi, monga kunyamula cihema copatulika na katundu wake pamene anali kucisamutsa. (Num. 4:46-49) Mlevi akakwanitsa zaka 25 anali kugwilako nchito zina, koma zioneka kuti nchitozo sizinali kukhala zolemetsa, monga nchito yosamutsa cihema copatulika. (Num. 8:24) M’nthawi ya Mfumu Davide, zaka za Alevi zoyamba utumiki wawo zinacepetsedwa kufika pa 20. Davide anakamba kuti cifukwa cimene anacitila zimenezo n’cakuti cihema copatulika sicidzanyamulidwanso (cifukwa cinali kudzaloŵedwa m’malo na kacisi). Utumiki unali kutha Mlevi akakwanitsa zaka 50. (Num. 8:25, 26; 1 Mbiri 23:24-26) Alevi anafunika kucidziŵa bwino Cilamulo, cifukwa nthawi zambili anali kuuzidwa kuti akaŵelenge Cilamuloco pagulu komanso kukaciphunzitsa kwa anthu.—1 Mbiri 15:27; 2 Mbiri 5:12; 17:7-9; Neh. 8:7-9.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w06 8/1 23 ¶13
Khalani Anzelu mwa Kuopa Mulungu
13Cifukwa cothandizidwa na Yehova panthawi ya mavuto, Davide anakulitsa khalidwe la kuopa Mulungu na kum’dalila. (Salimo 31:22-24) Komabe katatu konse Davide anabwelela m’mbuyo pa kuopa Mulungu ndipo anagwela m’mavuto oopsa. Nthawi yoyamba iye anakonza zoti likasa la cipangano ca Yehova lipite ku Yerusalemu pa galeta m’malo moti Alevi alinyamule pa mapewa pawo, monga mmene Cilamulo ca Mulungu cinanenela. Uza, amene anali kutsogolela galetalo, atagwila likasa lija kuti alikhazike bwino-bwino, anafela pomwepo cifukwa ca “kucita cinthu cosalemekeza Mulungu cimeneci.” Inde, Uza anacimwa kwambili, koma kweni-kweni iye analangidwa cifukwa cakuti Davide anacita zosalemekeza Cilamulo ca Mulungu. Kuopa Mulungu kumatanthauza kucita zinthu mogwilizana na njila imene Mulungu amacitila zinthu.—2 Samueli 6:2-9; Numeri 4:15; 7:9.
FEBRUARY 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 5-6
“Kodi Mungatengele Bwanji Citsanzo ca Anazili?”
it-2 477
Mnazili
Pali zinthu zitatu zikulu-zikulu zimene anthu ocita lumbilo la unaziri anali kuletsedwa kucita. Zinthuzo zinali: (1) Sanali kuloledwa kumwa coledzeletsa ciliconse. Komanso sanali kuloledwa kudya ciliconse cocokela ku mtengo wa mpesa, kaya mphesazo zikhale zosapsa, zakupsa, kapena zouma. Sanalinso kuloledwa kumwa madzi alionse ocokela ku mpesa, kaya osaŵila, oŵila, kapena viniga. (2) Sanali kuloledwa kumeta tsitsi lawo la kumutu. (3) Sanali kuloledwa kukhudza mtembo, ngakhale wa wacibale wapafupi kwambili, monga atate awo, amayi awo, m’bale wawo, kapena mlongo wawo.—Num. 6:1-7.
Malumbilo Apadela. Munthu amene wacita lumbilo lapadela limeneli, ‘anali kukhala Mnazili [kutanthauza, kudzipatulila] kwa Yehova,’ osati n’colinga cakuti anthu amutamande poona kuti amacita zinthu modzimana kwambili. M’malomwake, iye anali kukhala “woyela kwa Yehova masiku onse a Unaziri wake.”—Num. 6:2, 8; yelekezelani na Gen. 49:26.
Conco malamulo amene anapelekedwa kwa Anazili anali na tanthauzo lapadela pa kulambila Yehova. Mofanana na mkulu wa ansembe, amene cifukwa ca udindo wake wopatulika, sanali kuloledwa kukhudza mtembo wa munthu aliyense, ngakhale wa m’bale wake wapafupi kwambili, nawonso Anazili sanali kuloledwa kucita zimenezo. Mkulu wa ansembe pamodzi na ansembe aang’ono, cifukwa ca kukula kwa maudindo awo, anali kuletsedwa kumwa vinyo kapena cakumwa ciliconse coledzeletsa pogwila nchito zawo zopatulika pamaso pa Yehova.—Lev. 10:8-11; 21:10, 11.
Kuwonjezela apo, Mnazili (m’Ciheberi, na·zirʹ) “anali kukhala woyela mwa kusiya tsitsi lake kuti likule.” Ici cinathandiza onse kudziŵa mwamsanga kuti iwo anali Anazili oyela. (Num. 6:5) Liwu limodzi-modzili la Ciheberi lakuti na·zirʹ anali kuliseŵenzetsa pokamba za mitengo ya mphesa ‘yosadulila’, pa nthawi ya Sabata lopatulika ndiponso Zaka za Ufulu. (Lev. 25:5, 11) Kacitsulo kaphanthi-phanthi kagolide, kokhala patsogolo pa nduŵila ya mkulu wa ansembe, kanali na mawu olembedwa mocita kugoba akuti “Ciyelo n’ca Yehova.” N’zocititsa cidwi kuti kacitsuloka kanali kuchedwa “cizindikilo copatulika ca kudzipeleka,” [m’Ciheberi, neʹzer, liwu locokela ku magwelo amodzi na liwu lakuti na·zirʹ].” (Eks. 39:30, 31) Mofananamo, covala ca kumutu capadela kapena cisoti cacifumu cimene mafumu odzozedwa a Isiraeli ana kuvala, cinali kuchedwanso neʹzer. (2 Sam. 1:10; 2 Maf. 11:12) Mtumwi Paulo anakamba kuti mumpingo wacikhristu, mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali m’malo mwa covala kumutu. Tsitsilo ni cikumbutso kwa iye cakuti ali pa malo osiyana na mwamuna. Iye ayenela kukumbukila kuti afunika kugonjela makonzedwe a Mulungu. Conco malamulo akuti Anazili asamagele tsitsi, (zimene n’zosagwilizana na cikhalidwe ca amuna), asamamwe vinyo, komanso azikhala oyela ndi osadetsedwa, anali kukumbutsa Anazili odzipatulilawo za kufunika kokhala odzimana komanso kukhala ogonjela kothelatu ku cifunilo ca Yehova.—1 Akor. 11:2-16.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w05 1/15 30 ¶2
Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Koma Samisoni anali Mnazili wamtundu wina. Iye asanabadwe, mngelo wa Yehova anauza amayi ake kuti: “Pakuti udzatenga pakati ndi kubeleka mwana wamwamuna. M’mutu mwake musadzadutse lezala cifukwa mwanayo adzakhala Mnazili wa Mulungu potuluka m’mimba. Iye adzakhala patsogolo populumutsa Isiraeli m’manja mwa Afilisiti.” (Oweruza 13:5) Samisoni sanalumbile kukhala Mnazili. Mulungu ndiye anam’sankha kuti akhale Mnazili, ndipo anayenela kukhala Mnazili moyo wake wonse. Lamulo loletsa kukhudza mtembo silikanagwila nchito kwa iyeyo. Likanakhala logwila nchito kwa iyeyo ndiye kuti ngati akanakhudza mtembo mwangozi, kodi zikanatheka bwanji kuti ayambilenso moyo wake wokhala Mnazili umene unayambila pa kubadwa kwake? Motelo, zikuoneka kuti malamulo a anthu okhala Anazili kwa moyo wawo wonse anali kusiyanako ndi malamulo a Anazili ocita kungodzipeleka kwa kanthawi.