LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 7/1 tsa. 7
  • Zimene Mulungu Adzacita Pothetsa Zinthu Zoipa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Mulungu Adzacita Pothetsa Zinthu Zoipa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • N’cifukwa Ciani Zinthu Zoipa Zimacitikila Anthu Abwino?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • N’cifukwa Ciani Pa Dziko Pali Mavuto Ambili Conco?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Mulungu Ali Nalo Colinga Canji Dziko Lapansi?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Mavuto Adzatha Posacedwapa!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 7/1 tsa. 7

NKHANI YA PACIKUTO | N’CIFUKWA CIANI ZINTHU ZOIPA ZIMACITIKILA ANTHU ABWINO?

Zimene Mulungu Adzacita Pothetsa Zinthu Zoipa

Baibulo limatiuza momvekela bwino zimene Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu, adzacita ndi mavuto amene Satana Mdyelekezi amacititsa. Limati: “Mwana wa Mulungu [Yesu] anaonekela kuti aononge nchito za Mdyelekezi.” (1 Yohane 3:8) Dongosolo la zinthu lamakono limene ndi ladyela, cidani ndi macitidwe ena oipa lidzaonongedwa. Ponena za “wolamulila wa dzikoli,” Satana Mdyelekezi, Yesu analonjeza kuti ‘adzaponyedwa kunja tsopano.’ (Yohane 12:31) Popanda cisonkhezelo ca Satana dziko latsopano lolungama lidzakhazikitsidwa, ndipo padzikoli padzakhala mtendele wokhawokha.—2 Petulo 3:13.

Nanga bwanji za aja amene mwadala amakana kusintha njila zao ndipo amangopitilizabe kucita zinthu zoipa? Ganizilani lonjezo ili losapita m’mbali lakuti: “Oongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda colakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzacotsedwa padziko lapansi ndipo acinyengo adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) Anthu oipa sadzakhalaponso kuti acite zoipa. M’dziko lamtendele limenelo, anthu omvela adzamasuka pang’onopang’ono ku ucimo.—Aroma 6:17, 18; 8:21.

M’dziko latsopano, Mulungu adzathetsa bwanji zinthu zoipa? Sadzacita zimenezi mwakulanda anthu mphatso ya ufulu wodzisankhila zocita, kuti akhale monga makina amene amangocita zimene anapangidwila. Komabe, adzaphunzitsa anthu omvela njila zake, ndi kuwathandiza kusintha maganizo ao ndi zocita zao zoipa.

Mulungu adzacotsapo zinthu zonse zimene zimacititsa mavuto

Kodi Mulungu adzacitanji ndi ngozi zosayembekezeleka? Iye walonjeza kuti posacedwapa boma la Ufumu lidzayamba kulamulila dziko lapansi. Mfumu yoikidwa ndi Mulungu ya Ufumu umenewu ndi Yesu Kristu, amene ali ndi mphamvu yocilitsa odwala. (Mateyu 14:14) Yesu nayenso ali ndi mphamvu zolamulila cilengedwe. (Maliko 4:35-41) Conco, mavuto onse amene amacitika cifukwa ca “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka” adzatha. (Mlaliki 9:11) Mu ulamulilo wa Kristu, anthu sadzavutika ndi mavuto alionse.—Miyambo 1:33.

Nanga bwanji za anthu mamiliyoni osalakwa amene anafa pangozi? Yesu ali pafupi kuukitsa bwenzi lake Lazaro, anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Ndithudi, Yesu ali ndi mphamvu zoukitsa akufa kuti akhalenso ndi moyo.

Ngati mfundo yakuti anthu abwino sadzakumananso ndi mavuto yakukondweletsani, bwanji osayamba kuphunzila Baibulo kuti mudziŵe za Mulungu woona ndi cifuno cake? Mboni za Yehova kudela lanu n’zokonzeka kukuthandizani kupeza cidziŵitso cimeneci. Mwacikondi tikukupemphani kuti muwafikile kudela lanulo kapena lembelani ofalitsa magazini ino.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani