LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 January tsa. 13
  • Zimene Tingaphunzile kwa Samueli

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Tingaphunzile kwa Samueli
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Akamba na Samueli
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Samueli Sanaleke Kucita Zabwino
    Phunzitsani Ana Anu
  • Kamnyamata Kotumikila Mulungu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 January tsa. 13
Zithunzi: Zithunzi za m’vidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzile kwa Iwo—Samueli.” 1. Danny. 2. Samueli wacicepele.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Zimene Tingaphunzile kwa Samueli

Samueli anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova moyo wake wonse. Pamene anali wacicepele anakana kutengela makhalidwe oipa a ana a Eli, Hofeni na Pinihasi. (1 Sam. 2:22-26) Samueli anapitiliza kukula, ndipo Yehova anakhalabe naye. (1 Sam. 3:19) Ngakhale ku ukalamba wake, Samueli anapitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika ngakhale kuti ana ake anali osakhulupilika.—1 Sam. 8:1-5.

Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Samueli? Ngati ndinu wacicepele, dziŵani kuti Yehova amamvetsa mavuto amene mumakumana nawo komanso mmene mumamvelela. Iye angakuthandizeni kukhala wolimba mtima. (Yes. 41:10, 13) Ngati ndinu kholo ndipo mwana wanu analeka kutumikila Yehova, mungalimbikitsidwe kudziŵa kuti Samueli sanakakamize ana ake kutsatila miyezo ya Yehova. Iye anasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova, ndipo anapitiliza kusunga umphumphu wake, moti Atate wake Wakumwamba Yehova anakondwela naye. Mukakhala wokhulupilika, mwina citsanzo canu cabwino cidzasonkhezela mwana wanu kubwelela kwa Yehova.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE TINGAPHUNZILE KWA IWO—SAMUELI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzile kwa Iwo—Samueli.” Samueli wacicepele wanyamula nkhuni m’bwalo la cihema.

    Kodi Samueli anaonetsa bwanji kulimba mtima ali kamnyamata?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzile kwa Iwo—Samueli.” Danny wafikila mkulu wake ndipo akumufunsa za umoyo wapaŵili umene iye ali nawo.

    Kodi Danny anaonetsa bwanji kulimba mtima?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzile kwa Iwo—Samueli.” Mneneli Samueli ali wokalamba.

    Kodi Samueli anapeleka bwanji citsanzo cabwino pamene anali wokalamba?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Zimene Tingaphunzile kwa Iwo—Samueli.” Makolo ake a Danny pambuyo pocita ulaliki wapoyela na Danny.

    Yehova amawacilikiza anthu amene sasunthika pocita zabwino

    Kodi makolo a Danny anapeleka bwanji citsanzo cabwino?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani