NYIMBO 106
Kukulitsa Mkhalidwe wa Cikondi
Yopulinta
	- 1. Tithandizeni kuonetsa - Makhalidwe anu abwino. - Koposa zonse tionetse - Cikondi kwa abale athu. - Ngati cikondi cazilala, - Inu Yehova simukondwa. - Tionjezeleni cikondi, - Nthawi zonse ticionetse. 
- 2. Cikondi cimatipangitsa - Kuti tiganizile ena. - Tikhululukila anzathu, - Monga Yesu anakambila. - Cikondi cimatithandiza - Kupilila pamayeselo. - Cikondi cipilila zonse - Cikondi sicidzalephela. 
(Onaninso Yoh. 21:17; 1 Akor. 13:13; Agal. 6:2.)