MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO
Misonkhano ya Mpingo ya pa Vidiyo Konfalensi
JUNE 26, 2020
Maboma ambili padzikoli apeleka malangizo akuti anthu azikhala motalikilana komanso aletsa anthu kusonkhana pamodzi. Mboni za Yehova zifuna kuyesetsa kutsatila malangizo amenewa, koma panthawi imodzi-modziyo zifuna kupitilizabe kucita misonkhano m’njila imene siingaike miyoyo yawo kapena ya ena paciwopsezo. Kuti izi zitheke, mipingo yakhala ikucita misonkhano poseŵenzetsa zida (ma app) za vidiyo konfalensi monga Zoom.
Kuti mipingo izikwanitsa kucita misonkhano motetezeka nthawi zonse, Bungwe Lolamulila linavomeleza kugulila mipingo ma akaunti a Zoom poseŵenzetsa zopeleka za gulu. Izi zakhala zothandiza kwambili ku mipingo imene siikanakwanitsa kugula akaunti ya vidiyo konfalensi, imene imagulitsidwa madola 15 mpaka 20 kapena kuposelapo. Nthawi zambili mipingo imeneyo inali kuseŵenzetsa ma app aulele, amene amalola ciŵelengelo cocepa ca anthu kulumikiza ndiponso alibe citetezo cokwanila. Koma tsopano mipingo yonse imene imaseŵenzetsa ma akaunti a gulu imapindula cifukwa njila zake zacitetezo n’zosavuta, ndipo amalola kulumikiza anthu ambili ku msonkhano. Pano tikamba, mipingo yoposa 65,000 m’maiko oposa 170 imaseŵenzetsa ma akaunti amenewa.
Mpingo wa Kairagi wa m’dela la Manado, ku North Sulawesi, m’dziko la Indonesia, unaleka kuseŵenzetsa app yaulele ya vidiyo konfalensi n’kuyamba kugwilitsila nchito akaunti ya gulu ya Zoom. M’bale Hadi Santoso anati: “Ngakhale abale na alongo amene sadziŵa bwino kuseŵenzetsa zipangizo zamakono lomba akupindula na misonkhano. Izi zatheka maka-maka cifukwa cakuti safunikila kuloŵa na kutuluka maulendo angapo pa msonkhano umodzi.”
M’bale Lester Jijón, Jr., mkulu mumpingo wa Guayacanes Oeste ku Guayaquil, m’dziko la Ecuador, anati: “Cifukwa cakuti abale na alongo athu ambili ni osauka, mipingo ina siikanakwanitsa kugula akaunti ya Zoom imene ikanathandiza kuti mpingo wonse uzilumikiza ku misonkhano. Koma cifukwa cakuti timaseŵenzetsa ma akaunti a gulu a Zoom, tsopano n’zotheka kuitanilako ena momasuka ku misonkhano yathu, popanda kukhala na nkhawa yakuti ciŵelengelo ca olumikiza cidzapitilila malile.”
M’bale Johnson Mwanza, mkulu mumpingo wa Ngwerere North ku Lusaka, Zambia, analemba kuti: “Kaŵili-kaŵili abale na alongo ambili amakamba kuti, ‘kugwilitsila nchito ma akaunti a gulu a Zoom kumatithandiza kuona kuti tili pafupi na abale na alongo athu komanso kuti Yehova amatikonda na kutisamalila.’”
Ma akaunti a gulu amagulidwa na ndalama zimene zimasungidwa padela kuti zizithandiza pakagwa masoka. Ndalama zimenezo zimacokela pa zopeleka za nchito ya padziko lonse. Zambili mwa zopelekazo zimapelekedwa kupitila pa donate.jw.org. Tikuyamikilani ngako cifukwa ca zopeleka zanu zimene mumapeleka mowoloŵa manja. Zopelekazi zimagwilitsidwanso nchito pothandiza anthu okhudzidwa na masoka ena padziko lonse lapansi.—2 Akorinto 8:14.