NYIMBO 144
Yang’ana pa Mphoto
Yopulinta
(2 Akorinto 4:18)
1. Osaona adzaonanso.
Ndipo osamvela ‘dzamvela.
Ana adzaimba mokondwa.
Tidzakhala pamtendele.
Akufa adzaukitsidwa.
Adzakhala m’dziko labwino.
(KOLASI)
Iwe udzaonadi izi—
Ukayang’ana pamphoto.
2. Mimbulu na mkango na nkhosa,
Zidzadya pamodzi na ng’ombe.
Mwana adzazitsogolela,
Ndipo zidzamumvelela.
Zoŵaŵa, misozi na mantha,
Na kuvutika zidzasila.
(KOLASI)
Iwe udzaonadi izi—
Ukayang’ana pamphoto.
(Onaninso Yes. 11:6-9; 35:5-7; Yoh. 11:24.)