NYIMBO 6
Zakumwamba Zilengeza Ulemelelo wa Mulungu
Yopulinta
(Salimo 19)
1. Zakumwamba zitamanda Yehova.
Zilengeza mphamvu
zake zodabwitsa.
Dzuŵa, mwezi na nyenyezi zonse
Zimationetsa nzelu
Na cikondi cake.
2. Malamulo a M’lungu ni angwilo,
Amapatsa moyo
kwa oŵatsatila.
Ziweluzo zake n’zolungama.
Mau ake ni oyela,
Amatsitsimula.
3. Tingakhale na moyo wamuyaya,
Ngati ’se tiopa
Atate Yehova.
Kumumvela kumatiteteza.
Tiyeni tizilengeza.
Ucifumu wake.
(Onaninso Sal. 111:9; 145: 5; Chiv. 4:11.)