NYIMBO 46
Tikuyamikani Yehova
Yopulinta
(1 Atesalonika 5:18)
1. Tiyamikila Yehova Mulungu,
Munatipatsa kuwala kwanu.
Tiyamikila mwayi wa pemphelo,
Wokuuzani mavuto athu.
2. Tiyamikila munatuma Yesu,
Anapilila mpaka mapeto.
Tiyamikila mumatithandiza,
Kucita zimene mumafuna.
3. Tiyamikila potipatsa mwayi,
Wouza anthu za dzina lanu.
Tiyamikila za Ufumu wanu,
Kuti udzaleta madalitso.
(Onaninso Sal. 50:14; 95:2; 147:7; Akol. 3:15.)