NYIMBO 133
Lambila Yehova Ukali Wacicepele
Yopulinta
(Mlaliki 12:1)
1. Ise anyamata na ‘tsikana,
Yehova atikonda kwambili.
Atisamalila mwacikondi;
Adzadalitsa masiku athu.
2. Polemekeza makolo athu,
Tionetsa kuti tiŵakonda.
Ndipo Yehova adzatiyanja.
Iye adzakhala bwenzi lathu.
3. Tikumbukile Yehova M’lungu,
M’nthawi ya ucicepele wathu.
Tim’tumikile na moyo wonse,
Tidzakondweletsa mtima wake.
(Onaninso Sal. 71:17; Malilo 3:27; Aef. 6:1-3.)