NYIMBO 65
Pita Patsogolo!
Yopulinta
(Aheberi 6:1)
1. Pita patsogolo mu ulaliki!
Walitsa co’nadi kuti onse aone.
Ukhale na luso polalikila;
Udalile Yehova.
Nchito iyi ni yathu tonse;
Na Yesu analalikila.
Ukadalila Mulungu, sudzagwa.
Udzakhala wolimba.
2. Pita patsogolo, ucilimike!
Ulalikile uthenga kwa anthu onse.
Polalikilabe khomo ndi khomo,
Utamande Yehova.
Olo adani akuyofye,
Usayope lalikilabe.
Lengeza za Ufumu wa Yehova;
Phunzitsa coonadi.
3. Pita patsogolo, ucite cangu.
Nola luso lako, ndipo udzapambana.
Mzimu wa Mulungu ukuthandize.
Udzapeza cimwemwe.
Konda anthu omwe upeza,
Kuti uwafike pamtima.
Iwo akakula mwakuuzimu,
Co’nadi cidzawala.
(Onaninso Afil. 1:27; 3:16; Aheb. 10:39.)