NYIMBO 8
Yehova Ndiye Pothaŵila Pathu
Yopulinta
(Salimo 91)
1. Yehova m’potaŵila,
Ise tim’dalila.
Iye amateteza;
Okhulupilika.
Mthunzi wake n’citetezo,
Sitiyopa ciliconse.
Iye ni linga lathu,
Ise sitidzacokamo.
2. Ngakhale ena agwe,
Ise tisayope.
Yehova M’lungu wathu
Adzakhala nafe.
Iye adzatiteteza;
Ku zoyofya zilizonse.
Iye adzatisunga,
Pansi pa mapiko ake.
3. Adzaticinjiliza
Ku misampha yonse.
Usana ndi usiku,
Adzatiteteza.
Ngakhale m’nthawi ya tsoka,
Ise tidalila Iye.
Yehova m’pothaŵila,
Samasiya anthu ake.
(Onaninso Sal. 97:10; 121:3, 5; Yes. 52:12.)