NYIMBO 48
Kuyenda ndi Yehova Tsiku na Tsiku
Yopulinta
(Mika 6:8)
1. Tiziyenda na Yehova,
Nthawi zonse modzicepetsa.
Apatsa cisomo cake,
Kwa osakila njila zake.
Iye mwa cikondi cake,
Adzatitsogolela.
Tidzipeleke kwa iye
Kuti timutumikile.
2. Mapeto ayandikila,
Ndipo Satana ni wokwiya.
Adani amatiyofya
Kuti tisayende na M’lungu.
M’lungu adzatithandiza
Kuti tiyende naye.
Titumikile Yehova
Mpaka umuyaya wonse.
3. Mwa Mau na mzimu wake,
Yehova amatithandiza.
Watipatsa mpingo wake;
Amamvela tikapemphela.
Yehova atithandiza
Kucita zoyenela.
Afuna poyenda naye
Tikhale odzicepetsa.
(Onaninso Gen. 5:24; 6:9; 1 Maf. 2:3, 4.)