NYIMBO 49
Tikondweletse Mtima wa Yehova
Yopulinta
(Miyambo 27:11)
1. Tikulonjezani M’lungu,
Tidzakutumikilani,
Ise timakukondani.
Tidzakukondweletsani.
2. Atate munatipatsa
Kapolo wanu wanzelu,
Kuti atisamalile,
Atiphunzitse za imwe.
3. Tipatseni mzimu wanu,
Kuti ‘se utithandize
Kulengeza dzina lanu,
Kucita zofuna zanu.
(Onaninso Mat. 24:45-47; Luka 11:13; 22:42.)