Nyimbo 153
Kodi Mumamvela Bwanji?
Daunilodi
(Aheberi 13:15)
Mumamvela bwanji
polalikila ena,
Na kuphunzitsa anthu
okonda co’nadi?
Ngati simuleka,
M’lungu adzadalitsa.
Mudzathandiza anthu
kudziŵa Yehova.
(KOLASI)
Ise timasangalala
kudzipeleka kwa M’lungu.
Ndipotu sitidzaleka
Kum’tamanda iye.
Mumamvela bwanji
kuona kuti anthu
Akumvetsela uthenga
wopatsa moyo?
Ena amakana,
safuna na kumvela.
Koma ise sitileka
kulalikila.
(KOLASI)
Ise timasangalala
kudzipeleka kwa M’lungu.
Ndipotu sitidzaleka
Kum’tamanda iye.
Mumamvela bwanji
kuona kuti M’lungu,
Adzakuthandizani
kuti mupambane?
Timalalikila
na kuphunzitsa anthu
Tifuna kuti
nawo akapulumuke.
(KOLASI)
Ise timasangalala
kudzipeleka kwa M’lungu.
Ndipotu sitidzaleka
Kum’tamanda iye.
(Onaninso Mac. 13:48; 1 Ates. 2:4; 1 Tim. 1:11.)