LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 1 tsa. 14
  • Cidziŵitso Cimene Cimatithandiza Kukhala Mabwenzi a Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cidziŵitso Cimene Cimatithandiza Kukhala Mabwenzi a Mulungu
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mlengi Wathu Ali na Dzina
  • Yehova Ni Mulungu Wacikondi
  • Yehova Ni Mulungu Wokhululuka
  • Yehova Amafuna Kuti Tizipemphela kwa Iye
  • Yehova Ni Wokonzeka Kukhululuka
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Ziphunzitso Zoona Ponena za Mulungu ndi Ziti?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Mulungu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Muzikhala Okonzeka Kukhululukila Ena
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Onaninso Zina
Galamuka!—2021
g21 na. 1 tsa. 14

Cidziŵitso Cimene Cimatithandiza Kukhala Mabwenzi a Mulungu

Sikuti Mlengi wathu ni mphamvu cabe yopanda moyo. Koma ni Mulungu weniweni amene ali na makhalidwe abwino. Ndipo amafuna kuti tim’dziŵe na kukhala naye paubwenzi. (Yohane 17:3; Yakobo 4:8) Ndiye cifukwa cake watiuza zambili zokhudza iye.

Mlengi Wathu Ali na Dzina

“Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.”—SALIMO 83:18.

Baibo imaphunzitsa kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona. Iye ndiye analenga cilengedwe conse na zamoyo zonse. Tiyenela kulambila iye cabe.—Chivumbulutso 4:11.

Yehova Ni Mulungu Wacikondi

Dzina la Mlengi lakuti, Yehova, lolembedwa m’ci Hindi, ci Punjabi, ci Gujarati, ci Telugu, ci Tamil, na Cinyanja.

“Mulungu ndiye cikondi.”—1 YOHANE 4:8.

Kupitila m’Baibo komanso zinthu zimene analenga, Yehova amatiphunzitsa makhalidwe ake ambili. Khalidwe lake lalikulu ni cikondi. Iye amacita zinthu zonse cifukwa ca cikondi. Tikaphunzila zambili za Yehova, timafika pom’konda kwambili.

Yehova Ni Mulungu Wokhululuka

“Inu ndinu Mulungu wokhululuka”—NEHEMIYA 9:17.

Yehova amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo. Conco amakhala wokonzeka kutikhululukila. Tikavomeleza kulakwa kwathu na kuyesetsa kuleka kucita zinthu zoipa, iye adzatikhululukila ndipo sadzatipatsanso cilango cifukwa ca macimo amene tinalapa.—Salimo 103:12, 13.

Yehova Amafuna Kuti Tizipemphela kwa Iye

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—SALIMO 145:18, 19.

Yehova safuna kuti pomulambila tizicita miyambo yapadela kapena kuseŵenzetsa mafano na zinthu zina. Iye amamvetsela mapemphelo athu monga mmene makolo acikondi amamvetselela ana awo akamakamba.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani