LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g24 na. 1 masa. 10-12
  • Kulemekezana m’Banja

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kulemekezana m’Banja
  • Galamuka!—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIFUKWA CAKE KULEMEKEZANA M’BANJA N’KOFUNIKA
  • ZIMENE MUNGACITE
  • ZIMENE IFE MBONI TIMACITA
  • Thandizo Ilipo
    Galamuka!—2020
  • 12 Zolinga
    Galamuka!—2018
  • Pezani Nzelu Zothandiza pa Umoyo pa JW.ORG
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Onaninso Zina
Galamuka!—2024
g24 na. 1 masa. 10-12
Mwamuna wokhumudwa ali pa foni yake pamene mkazi wake akufuna kukamba naye. Ndipo mwana wawo wamng’ono akuona.

Kulemekezana m’Banja

CIFUKWA CAKE KULEMEKEZANA M’BANJA N’KOFUNIKA

Kulemekezana m’banja kumapangitsa kuti mukhale mtendele, ndipo amuna, akazi, komanso ana amaona kuti ni osungika.

  • Buku lakuti The Seven Principles for Making Marriage Work linati okwatilana amene amapatsana ulemu amaonetsana cikondi “osati cabe mwa kucitilana zinthu zikulu-zikulu, koma ngakhale zing’ono-zing’ono tsiku lililonse.”

  • Kafukufuku aonetsa kuti ana amene amaphunzila kulemekeza ena amadziona moyenela, amakhala pa ubwenzi wabwino na makolo awo, ndiponso savutika kaŵili-kaŵili na matenda a maganizo.

ZIMENE MUNGACITE

Pangani pulani na banja lanu. Coyamba, onetsetsani kuti aliyense akudziŵa zimene “ulemu” umatanthauza. Caciŵili, lembani makhalidwe amene aliyense m’banja ayenela kuonetsa komanso amene ayenela kupewa. Cacitatu, kambilanani za pulaniyo monga banja n’colinga cakuti ana anu komanso inuyo mudziŵe zocita kuti muzionetsa ulemu.

“Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendele bwino.”—Miyambo 21:5.

Khalani citsanzo cabwino. Kodi mumakonda kudzudzula a m’banja lanu pa zimene amalakwitsa, kusuliza maganizo awo, kusukulutsa zokamba zawo kapena kuwadula mawu pamene akukamba namwe?

Yesani izi: Muziona kuti ni udindo wanu kupatsa ulemu mnzanu wa mu ukwati komanso ana anu. Muziwalemekeza kaya muona kuti ni oyenela kupatsidwa ulemu kapena ayi.

“Pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.”—Aroma 12:10.

Khalanibe aulemu ngakhale pamene muli ndi maganizo osiyana ndi a munthu winayo. Pamene mufotokoza maganizo anu, pewani kukamba mawu monga akuti, “iwe nthawi zonse umakonda” kapena “iwe sumacita zakuti-zakuti.” Mawu olasa ngati amenewa angakhumudwitse a m’banja mwanu ndipo angapangitse nkhani yaing’ono kukula n’kukhala mkangano.

“Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”—Miyambo 15:1.

Mtsikana akutamba vidiyo pa jw.org.

ZIMENE IFE MBONI TIMACITA

Mboni za Yehova zimalimbikitsa mabanja kumacitilana zinthu mwaulemu. Ndipo pali nkhani zambili zolimbikitsa ulemu m’mabanja m’mabuku, m’mabulosha, m’mavidiyo komanso m’nkhani zina zimene timafalitsa kwaulele.

KWA OKWATILANA: Nkhani zakuti Mfundo Zothandiza Mabanja zingathandize amuna na akazi . . .

  • kukhala amvetseli abwino

  • kusasiya kulankhulana akasemphana maganizo

  • kupewa kukangana

(Fufuzani mawu akuti “Mfundo Zothandiza Mabanja” pa jw.org ku Chichewa)

KWA MAKOLO: Nkhani zakuti Mfundo Zothandiza Mabanja zingathandize makolo kuphunzitsa ana awo . . .

  • kukhala omvela

  • kugwila nchito za pa khomo

  • kukhala aulemu komanso oyamikila

(Fufuzani mawu akuti “Kulera Ana” komanso “Kulera Ana Achinyamata” pa jw.org ku Chichewa)

Onaninso zakumapeto, “Mafunso Amene Makolo Amadzifunsa,” m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba. (Fufuzani mawu akuti “Mafunso Amene Makolo Amadzifunsa” pa jw.org ku Chichewa)

KWA ACINYAMATA: Mbali yakuti Achinyamata pa jw.org ku Chichewa ili na nkhani, mavidiyo komanso zocita zimene zingathandize acinyamata kuti . . .

  • azigwilizana na makolo komanso ana anzawo m’banja

  • azikambilana mwaulemu na makolo awo pa nkhani ya malamulo a pabanja

  • kucita zinthu zopangitsa makolo awo kuwadalila

(Fufuzani mawu akuti “Achinyamata” pa jw.org ku Chichewa)

Webusaiti ya jw.org ni yaulele. Simufunika kulipila ndalama iliyonse, kulembetsa, kapena kukhala membala kuti muiseŵenzetse. Simudzapemphedwa kutumiza zilizonse zokhudza inu.

Joseph Ehrenbogen.

DZIWANI ZAMBILI

Pamene Joseph Ehrenbogen anakwatila, anali waciwawa komanso anali na cizolowezi cogwilitsa nchito mankhwala osokoneza bongo. Kuti mudziŵe mmene kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova kunasinthila umoyo wake komanso wa banja lake, fufuzani nkhani yakuti “Ndinaphunzila Kulemekeza Akazi Ndiponso Kudziona Moyenela” pa jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani