LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • kr nkhani 14 nkhani 148-156
  • Kucilikiza Boma la Mulungu Mokhulupilika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kucilikiza Boma la Mulungu Mokhulupilika
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Nkhani Yaikulu Imene Ikutikhudza
  • Zizunzo Zoopsa Zokhala Ngati “Mtsinje”
  • ‘Dziko’ Linameza “Mtsinje” Umenewo
  • Nkhani Yokhudza Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko
  • Kusakhala Mbali ya Dziko Kumabweletsa Mgwilizano
  • Kumenyela Ufulu wa Kulambila
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Alaliki a Ufumu Amapeleka Milandu Yao ku Khoti
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • “Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
kr nkhani 14 nkhani 148-156

NKHANI 14

Kucilikiza Boma la Mulungu Mokhulupilika

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Anthu a Mulungu sakhala mbali ya dziko cifukwa cakuti ndi okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu

1, 2. (a) Ndi mfundo iti imene otsatila a Yesu akhala akuitsatila? (b) Kodi adani athu akhala akucita ciani pofuna kutigonjetsa? Nanga cotulukapo cake cakhala ciani?

YESU ataimilila pamaso pa wolamulila wamphamvu waciyuda dzina lake Pilato, ananena mfundo imene otsatila ake oona akhala akuitsatila mpaka pano. Iye anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisapelekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wocokela pansi pano ayi.” (Yoh. 18:36) Pilato anapha Yesu, koma iye sanapambane cifukwa cakuti Yesu anaukitsidwa. Olamulila a Ufumu wamphamvu wa Roma anafuna kufafaniza otsatila a Kristu, koma zoyesayesa zao sizinaphule kanthu. Panthawiyo Akristu anafalitsa uthenga wa Ufumu padziko lonse lapansi.—Akol. 1:23.

2 Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa mu 1914, maulamulilo ena amphamvu kwambili anafuna kufafaniza anthu onse a Mulungu. Koma palibe ulamulilo umene wakwanitsa kutigonjetsa. Maboma ambili ndi magulu andale anayesa kutikakamiza kuti titenge nao mbali m’mikangano yao yandale. Colinga cao cinali cakuti atigawanitse, koma analephela. Masiku ano, nzika za Ufumu wa Mulungu zimapezeka pafupifupi m’dziko lililonse. Ngakhale zili conco, ndife ogwilizana, tili paubale weniweni wapadziko lonse, ndipo sitimatenga mbali m’ndale za dziko ngakhale pang’ono. Mgwilizano wathu ndi umboni wosatsutsika wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila, ndi kuti Mfumu Yesu Kristu ikupitilizabe kutsogolela nzika zake, kuziyenga, ndi kuziteteza. Tiyeni tikambilane mmene Yesu wacitila zimenezi ndi mmene watithandizila kuti tipambane milandu ina. Zipambano zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo cathu pamene tikupitilizabe kusakhala “mbali ya dziko.”—Yoh. 17:14.

Nkhani Yaikulu Imene Ikutikhudza

3, 4. (a) N’ciani cimene cinacitika panthawi imene Ufumu unabadwa? (b) Kodi anthu a Mulungu anali kuona kuti kusatenga mbali m’zandale kumatanthauza ciani?

3 Pambuyo pakuti Ufumu wabadwa, kumwamba kunabuka nkhondo. Ndiyeno Satana anaponyedwa padziko lapansi. (Ŵelengani Chivumbulutso 12:7-10, 12.) Padziko lapansi panabukanso nkhondo, ndipo nkhondoyo inayesa cikhulupililo ca anthu a Mulungu. Koma anthu a Mulungu anali otsimikiza mtima kutsatila citsanzo ca Yesu ndi kusakhala mbali ya dziko. Komabe, io poyamba sanali kudziŵa bwino cimene kusaloŵelela ndale kumatanthauza.

4 Mwacitsanzo, Voliyamu 6 ya buku lakuti Millennial Dawn,a imene inafalitsidwa mu 1904, inapeleka malangizo akuti Akristu sayenela kumenya nkhondo. Komabe, bukulo linafotokoza kuti ngati Mkristu analembedwa kale nchito ya usilikali, iye ayenela kugwila nchito imene siphatikizapo kumenya nkhondo. Ngati zimenezo zalepheleka, ndipo Mkristuyo watumizidwa ku nkhondo, bukulo linati iye ayenela kupewa kupha. Pothilila ndemanga pankhaniyi, m’bale Herbert Senior amene anali kukhala ku Britain, ndipo anabatizidwa mu 1905, anati: “Zimenezi zinabweletsa msokonezo waukulu pakati pa abale cifukwa cakuti panalibe malangizo omveka bwino osonyeza kuti Mkristu angaloŵe nchito ya usilikali kuti azigwila nchito imene siifuna kunyamula zida za nkhondo kapena ai.”

5. Kodi magazini ya The Watch Tower ya September 1, 1915, inamveketsa bwanji nkhani yokhudza kusatenga mbali m’zandale?

5 Komabe magazini ya The Watch Tower ya September 1, 1915, inayamba kumveketsa bwino nkhaniyi. Ponena za mfundo zimene zinalongosoledwa m’buku lakuti Studies in the Scriptures, magaziniyo inati: “Tikuganiza kuti kuloŵa nchito ya usilikali kapena kugwila nchito imene siifuna kunyamula zida za nkhondo ku usilikaliko, ndi kuphwanya mfundo zathu zacikristu.” Koma bwanji ngati Mkristu angauzidwe kuti adzaphedwa cifukwa cokana kuvala yunifomu ndi kugwila nchito yausilikali? Magaziniyo inafunsa kuti: “Kodi pali vuto ngati m’bale angaphedwe cifukwa cokhala wokhulupilika kwa Kalonga Wamtendele mwa kukana kuswa malamulo ake? Kapena kodi ndi bwino kuti m’bale aphedwe cifukwa cogwilila nchito mafumu a dziko ndi kuwacilikiza cimene cili cizindikilo cakuti m’baleyo wakana kutsatila ziphunzitso za Mfumu ya Kumwamba? Pa ziŵilizi, ife tingasankhe kufa cifukwa cokhala wokhulupilika kwa Mfumu yathu ya Kumwamba.” Ngakhale kuti magaziniyo inafotokoza mfundoyo mwamphamvu, inamaliza ndi mau akuti: “Sitikukakamiza munthu kutsatila zimenezi. Tikungopeleka malingalilo.”

6. Kodi mwaphunzilapo ciani pa citsanzo ca M’bale Herbert Senior?

6 Abale ena anamvetsa mfundoyi, ndipo anali okonzeka kukumana ndi mavuto cifukwa cokana kuloŵa usilikali. M’bale Herbert Senior amene tamugwila mau poyamba paja, anati: “Ine ndinali kuona kuti palibe kusiyana pakati pogwila nchito yotsitsa zipolopolo za mfuti m’bwato [nchito imene siphatikizapo kumenya nkhondo] ndi kuika zipolopolo mu mfuti kuti akaombele ku nkhondo.” (Luka 16:10) M’bale Senior anaikidwa m’ndende cifukwa cokana kuloŵa nchito ya usilikali kaamba ka cikumbumtima cake. M’baleyu ndi abale ena anai anali pakati pa anthu 16 amene anakana kuloŵa usilikali cifukwa ca cikumbumtima cao. Anthu 16 amenewa anali kuphatikizapo anthu a zipembedzo zina amene anali nao kundende ya ku Britain yochedwa Richmond. Panthawi ina, m’bale Senior ndi anthu ena anatengedwa mwacisinsi kupita nao ku malo a nkhondo ku France. Ali kumeneko, anauzidwa kuti adzaphedwa ndi mfuti. M’baleyo ndi anthu ena anaikidwa kutsogolo kwa asilikali kuti awaphe ndi mfuti, koma sanawaphe. M’malo mophedwa, anauzidwa kuti adzakhala m’ndende zaka 10.

Simon Kraker

“Ndinadziŵa kuti anthu a Mulungu ayenela kukhala pa mtendele ndi wina aliyense ngakhale panthawi ya nkhondo.”—Simon Kraker (Onani ndime 7)

7. N’ciani cimene anthu a Mulungu anadziŵa pamene Nkhondo Yaciŵili Yapadziko Lonse inayamba?

7 Pamene Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse inayamba, anthu a Yehova anadziŵa bwino zimene kusaloŵelela m’ndale kumatanthauza, ndi zimene anafunika kucita kuti atsatile citsanzo ca Yesu. (Mat. 26:51-53; Yoh. 17:14-16; 1 Pet. 2:21) Mwacitsanzo, Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya November 1, 1939, inali ndi nkhani yapadela ya mutu wakuti, “Kusatenga Mbali m’Zandale.” Nkhaniyo inati: “Lamulo limene anthu a Yehova ayenela kutsatila tsopano ndi lakuti sayenela kutenga mbali m’nkhondo. Ponena za nkhaniyo, m’bale Simon Kraker, amene m’kupita kwa nthawi anadzatumikila ku likulu ku Brooklyn, New York, anati: “Ndinadziŵa kuti anthu a Mulungu ayenela kukhala pa mtendele ndi wina aliyense ngakhale panthawi ya nkhondo.” Cakudya ca kuuzimu cimeneco cinapelekedwa panthawi yake, ndipo cinathandiza anthu a Mulungu kukonzekela mavuto oopsa amene anayesa kukhulupilika kwao ku Ufumu wa Mulungu.

Zizunzo Zoopsa Zokhala Ngati “Mtsinje”

8, 9. Kodi ulosi wa mtumwi Yohane unakwanilitsidwa bwanji?

8 Mtumwi Yohane analosela kuti pambuyo pakuti Ufumu wabadwa mu 1914, cinjoka, kapena kuti Satana Mdyelekezi, cidzayesa kufafaniza anthu ocilikiza Ufumu wa Mulungu mwa kulavula mtsinje wophiphilitsa kucokela m’kamwa mwake.b (Ŵelengani Chivumbulutso 12:9, 15.) Kodi ulosi wa Yohane umenewo unakwanilitsidwa bwanji? Kuyambila ca m’ma 1920, anthu a Mulungu anakumana ndi zinzunzo zambili zosiyanasiyana. Mofanana ndi abale ambili amene anali kukhala ku North America panthawi ya nkhondo yaciŵili yapadziko lonse, M’bale Kraker anaikidwa m’ndende cifukwa cokhala wokhulupilika ku Ufumu wa Mulungu. Pamene nkhondoyi inali mkati, a Mboni za Yehova ndi amene anali oculuka m’ndende za ku United States. Iwo anaimbidwa mlandu wokana kumenya nkhondo cifukwa ca cikhulupililo cao.

9 Mdyelekezi ndi anthu ake anali otsimikiza mtima kupangitsa nzika za Ufumu kuti zisiye kukhala zokhulupilika kwa Mulungu mosasamala kanthu kumene zinali kukhala. M’maiko ambili mu Africa, ku Europe, ndi ku United States, abale oculuka anawapeleka ku makhoti ndi kwa anthu oona zokhululukila milandu ya akaidi. Popeza kuti abale athu anakanitsitsa kuloŵa ndale, io anaikidwa m’ndende, anamenyedwa ndi kuvulazidwa mpaka ena analemala. Ku Germany, anthu a Mulungu anakumana ndi mavuto ambili cifukwa cokana kunena mau otamanda Hitler kapena kumenya nkhondo. Anthu oposa 6,000 anaikidwa m’ndende panthawi ya ulamulilo wa Nazi, ndipo Mboni za Yehova zoposa 1,600 za ku Germany ndiponso zocokela ku maiko ena zinaphedwa ndi anthu akhanza amenewo. Ngakhale zinali conco, Mdyelekezi sanakwanitse kufafanizilatu anthu a Mulungu.—Maliko 8:34, 35.

“ANAFA CIFUKWA COPELEKA ULEMELELO KWA MULUNGU”

Gerhard Steinacher

PAMENE nkhondo yaciŵili ya padziko lonse inali mkati, Mboni za Yehova zinali zocepa ku Germany, panthawi ya ulamulilo wa Nazi. Koma wolemba mbili wina dzina lake Detlef Garbe analemba kuti ngakhale zinali conco, “a Mboni za Yehova ndi amene anali ambili pakati pa anthu amene anapatsidwa mlandu ndi asilikali wokana kumenya nkhondo cifukwa ca cikumbumtima cao . . . m’nthawi ya ulamulilo wa Hitler.” Mmodzi wa anthu amene anapatsidwa mlandu umenewu anali Gerhard Steinacher wa ku Austria amene anali ndi zaka 19. Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itangoyamba, akuluakulu a ulamulilo wa Nazi anagwila m’baleyu cifukwa cokana kukhala msilikali wa dziko la Germany.

Mu November 1939, m’bale Gerhard anaweluzidwa kuti ayenela kuphedwa. Mwezi umenewo, m’baleyu analemba kalata akali m’ndende. Iye anati: “Ndikungofuna kupeleka ulemelelo kwa Mulungu, kusunga malamulo ake, ndi kumupempha kuti akatilandile mu Ufumu wake, mmene mudzakhala moyo wamuyaya ndi mtendele.”

Pa March 29, 1940, kutangotsala tsiku limodzi kuti anyongedwe, m’bale Gerhard anatsanzika makolo ake ndi mau akuti: “Ndikali wamg’ono kwambili, koma ndidzacilimika pa ciyeso cimeneci Ambuye akandipatsa mphamvu, ndipo zimenezi ndi zimene ndikupempha kwa iye.” M’bale Gerhard ananyogedwa tsiku lotsatila ca m’ma 6 koloko m’mawa, ndipo mosakaikila anamupha mocita kum’dula mutu. Pa cikwangwani ca pamanda ake pali mau akuti: “Anafa cifukwa copeleka ulemelelo kwa Mulungu.”

‘Dziko’ Linameza “Mtsinje” Umenewo

10. Kodi “dziko lapansi” likuimila ciani? Nanga lathandiza bwanji anthu a Mulungu?

10 Ulosi umene mtumwi Yohane analemba unasonyeza kuti “dziko lapansi,” kutanthauza anthu ena m’dziko la Satanali, adzameza “mtsinje” wa cinzunzo ndi kuthandiza anthu a Mulungu. Kodi mbali ya ulosi imeneyi inakwanilitsidwa bwanji? Zaka zambili pambuyo pa Nkhondo Yaciŵili Yapadziko Lonse, “dziko lapansi” lakhala likuthandiza anthu amene amacilikiza Ufumu wa Mesiya mokhulupilika. (Ŵelengani Chivumbulutso 12:16.) Mwacitsanzo, makhoti ambili ochuka akhala akuteteza ufulu wa Mboni za Yehova wokana kuloŵa nchito ya usilikali kapena kucita miyambo yosonyeza kukonda dziko lao. Coyamba, onani milandu ina ikuluikulu yokhudza nchito ya usilikali imene Yehova wathandiza anthu ake kupambana.—Sal. 68:20.

11, 12. Kodi M’bale Sicurella ndi M’bale Thlimmenos anawapeza ndi mlandu wotani? Nanga zotsatilapo zake zinali zotani?

11 Ku United States. M’bale Anthony Sicurella analeledwa m’banja la Mboni. Iye anabatizidwa pamene anali ndi zaka 15. Pamene anafika zaka 21, iye analembetsa ku bungwe lokakamiza anthu kuloŵa usilikali kuti anali mtumiki wa Mulungu. Mu 1950, patapita zaka ziŵili, iye anapitanso ku bungwelo kukalembetsa kuti safuna kuloŵa usilikali cifukwa ca cikumbumtima cake. Ngakhale kuti bungwe lofufuza milandu lochedwa Federal Bureau of Investigation silinaone colakwika ndi cosankha ca m’baleyo, Dipatimenti Yoona za Cilungamo m’dzikolo inakana pempho lake. Pambuyo pakamba nkhaniyo kangapo m’khoti laling’ono, Khoti Lalikulu la ku America linaweluzanso nkhani ya M’bale Sicurella. Khotilo linasintha cigamulo ca khoti laling’ono mwa kuweluza mlandu mokomela m’baleyo. Cigamuloco cinathandizanso nzika zina za ku United States zimene zinali kukana kuloŵa nchito ya usilikali cifukwa ca cikumbumtima cao.

12 Ku Greece. Mu 1983, M’bale Iakovos Thlimmenos anaimbidwa mlandu wakuti anali wamwano cifukwa cakuti anakana kuvala yunifomu ya usilikali, ndipo anaikidwa m’ndende. Pambuyo pomasulidwa, m’baleyo anafuna kuloŵa nchito yoŵelenga ndalama, koma olemba nchito anam’kana cifukwa cakuti anali ndi mlandu wakuti ndi wophwanya malamulo. Anapititsa nkhaniyo ku makhoti a m’dzikolo, koma sanaweluze mlandu wake mom’komela. Pambuyo pake iye anapititsa mlandu wake ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Mu 2000, oweluza 17 a m’Komiti Yaikulu ya Khotilo anaweluza mlandu wa M’bale Thlimmenos mom’komela, ndipo ciweluzoco cinakhala monga citsanzo pa milandu ina yokhudza tsankho. Cigamulo ca nkhaniyo cisanapelekedwe, abale oposa 3,500 ku Greece amene anakhalako m’ndende cifukwa cokana kuloŵa usilikali, anali ndi milandu yakuti anali anthu ophwanya malamulo. Pambuyo pa cigamuloci, dziko la Greece linakhazikitsa lamulo limene linathandiza kuti abale onse amene anali kuimbidwa milandu yophwanya malamulo awafafanizile milandu yao yonse. Ndiponso lamulo lakuti nzika zonse za ku Greece zili ndi ufulu wogwila nchito zina zosakhala za usilikali limene linali litapelekedwa kale m’dzikolo, koma linali litasiya kugwila nchito, linayambanso kugwila nchito pamene anakonzanso malamulo a ku Greece.

Ivailo Stefanov

“Ndisanaloŵe m’khoti, ndinapemphela kwa Yehova mocokela pansi pamtima, ndipo iye anandithandiza kuti mtima wanga ukhale m’malo.”—Ivailo Stefanov (Onani ndime 13)

13, 14. Kodi tiphunzilapo ciani pa milandu yokhudza Ivailo Stefanov ndi Vahan Bayatyan?

13 Ku Bulgaria. Mu 1994, pamene Ivailo Stefanov anali ndi zaka 19, anauzidwa kuloŵa usilikali. Iye anakana kuloŵa usilikali kapena kugwila nchito zina zimene zinali kuyang’anilidwa ndi asilikali. Pa cifukwa cimeneci, anaweluzidwa kuti akhale m’ndende kwa miyezi 18, koma cifukwa cakuti anali ndi ufulu wokana kugwila nchito zina cifukwa ca cikumbumtima cake, iye anacita apilo mlandu wake. Mlandu wake unafika mpaka ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Koma khotilo lisanamve mlandu wa m’bale Stefanov mu 2001, boma la dzikolo linasintha cigamulo cake ndi kuweluzanso mlanduwo mokomela m’bale wathuyo. Boma la dziko la Bulgaria linafafaniza mlandu wa M’bale Stefanov kuphatikizapo milandu ya nzika zina za ku Bulgaria zimene zinali zokonzeka kugwila nchito zina zosakhala za usilikali.c

14 Ku Armenia. Mu 2001, M’bale Vahan Bayatyan, anafika pa msinkhu woloŵa usilikali mogwilizana ndi malamulo a dzikolo.d Iye anakana kuloŵa usilikali cifukwa ca cikumbumtima cake, koma makhoti onse a m’dzikolo anaweluza mlandu wake mosam’komela. M’baleyo anakhala m’ndende kuyambila mu September 2002, ndipo anafunika kukhala m’ndendemo kwa zaka ziŵili ndi hafu, koma anamasulidwa pambuyo pokhala m’ndende kwa miyezi 10 ndi hafu. Panthawiyo, m’bale Bayatyan anacita apilo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, ndipo linavomela kuweluza mlandu wake. Komabe pa October 27, 2009, Khotilo linaweluzanso mlanduwo mosakomela mbale wathu. Ciweluzoco cinali monga ndi kukhaulitsa abale athu a ku Armenia amene analinso ndi milandu yofanana ndi umenewu. Koma Komiti Yaikulu ya Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya inaweluzanso mlanduwo. Pa July 7, 2011, Khotilo linaweluza mlanduwo mokomela Vahan Bayatyan. Uwu unali ulendo woyamba pamene Khotilo linazindikila kuti liyenela kuteteza ufulu wa anthu amene safuna kugwila nchito za usilikali cifukwa ca cikhulupililo cao mogwilizana ndi ufulu wa maganizo, wa cikumbumtima ndi wa cipembedzo umene munthu aliyense ali nao. Cigamuloco cimateteza ufulu wa Mboni za Yehova komanso ufulu wa anthu mamiliyoni ambili amene amakhala ku maiko amene ndi mamembala a m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya.e

Abale ku Armenia atulutsidwa m’ndende

Abale ku Armenia atulutsidwa m’ndende pambuyo pa cigamulo cowakomela ca Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya

Nkhani Yokhudza Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko

15. N’cifukwa ciani anthu a Yehova amakana kucita nao miyambo yosonyeza kukonda dziko lao?

15 Anthu a Yehova amaonetsa kuti ndi okhulupilika ku Ufumu wa Mesiya mwa kukana kuloŵa usilikali, komanso pamene mwaulemu amakana kucita zikondwelelo zosonyeza kukonda dziko lao. Mzimu wokonda dziko lako wafala kwambili kuyambila panthawi ya Nkhondo Yaciŵili Yapadziko Lonse. Nzika za m’maiko ambili zimafunikila kulumbila posonyeza kuti zidzakhala zokhulupilika ku dziko lao mwa kunena mau ena ake pamtima, kuimba nyimbo ya fuko, kapena kucitila saliyuti mbendela. Komabe, ife timadzipeleka kwa Yehova yekha. (Eks. 20:4, 5) Pa cifukwa cimeneci, takhala tikukumana ndi zizunzo zambili. Ngakhale ndi conco, Yehova wakhala akugwilitsila nchito “dziko lapansi” kuthetsa zizunzo zina. Onani milandu ina yokhudza nkhani imeneyi yomwe Yehova watithandiza kupambana kupyolela mwa Kristu.—Sal. 3:8.

16, 17. Kodi Lillian ndi William Gobitas anawapeza ndi mlandu wotani? Nanga n’ciani cimene mwaphunzilapo pa mlandu wao?

16 Ku United States. Mu 1940, oweluza 8 pa oweluza 9 mu Khoti Lalikulu la ku United States anaweluza motsutsana ndi Mboni za Yehova pa mlandu umene unali pakati pa sukulu ya Minersville School District ndi banja la Mbale Gobitis. Pofuna kukhala wokhulupilika kwa Yehova, Lillian Gobitas,f wa zaka 12 ndi m’bale wake William wa zaka 10, anakana kucitila saliyuti mbendela ndi kunena mau apamtima osonyeza kukhulupilika ku dziko lao. Pa cifukwa cimeneci, anacotsedwa sukulu. Mlandu wao unapita ku Khoti Lalikulu la dzikolo. Khotilo linanena kuti zimene aphunzitsi a sukuluyo anacita zinali zogwilizana ndi malamulo a dzikolo cifukwa zinali zolimbikitsa “mgwilizano m’dziko.” Cigamuloco cinapangitsa kuti abale athu akumane ndi mavuto oopsa. Ana ambili a Mboni anacotsedwa sukulu, abale athu anacotsedwa nchito, ndipo Mboni zina zinamenyedwa koopsa ndi magulu a anthu akhanza. Buku lochedwa The Lustre of Our Country linati: “Mavuto amene a Mboni anakumana nao ku America kuyambila mu 1941 mpaka mu 1943, anali oopsa kwambili kuposa mavuto ena onse amene anacitika m’zaka za m’ma 1900 m’dzikolo.”

17 Cipambano ca adani a Mulungu cinali ca kanthawi kocepa cabe. Mu 1943, Khoti Lalikulu la dzikolo linaweluzanso mlandu wina wofanana ndi wa banja la M’bale Gobitis. Mlanduwo unali pakati pa Barnette ndi Oyang’anila Maphunzilo M’cigawo ca West Virginia. Panthawiyi, Khotilo linaweluza mlanduwo mokomela Mboni za Yehova. Aka kanali koyamba kuti Khoti Lalikulu ku United States lisinthe cigamulo cake m’kanthawi kocepa conco. Pambuyo pa cigamuloco, cizunzo cimene anthu a Yehova anali kukumana naco ku United States cinacepa kwambili. Ndipo cigamuloco cinathandiza kuti boma la dzikolo lizilemekeza ufulu wa nzika zake zonse.

18, 19. Kodi M’bale Pablo Barros anakamba kuti n’ciani cinam’thandiza kuti akhalebe wolimba? Kodi atumiki ena a Yehova angam’tsanzile bwanji?

18 Ku Argentina. Pablo Barros wa zaka 8 ndi Hugo Barros wa zaka 7, anacotsedwa sukulu mu 1976 cifukwa cokana kucita nao mwambo wokwezeka mbendela. Nthawi ina, mphunzitsi wamkulu pasukulupo anakankha Pablo ndi kumumenya pamutu. Mphunzitsiyo analamula anao kukhalila ku sukulu kwa ola lathunthu anzao ataweluka. Nthawi yonseyo anali kuwakakamiza kucita miyambo yosonyeza kukonda dziko lao. Pofotokoza mmene zinthu zinalili, Pablo anati: “Popanda thandizo la Yehova sindikanakwanitsa kukhala wokhulupilika kwa iye.”

19 Pamene nkhaniyo inapita ku khoti, woweluza mlanduyo anakamba kuti aphunzitsi a pa sukulupo anacita bwino kucotsa sukulu Pablo ndi Hugo. Komabe, abale anacita apilo nkhaniyo ku Khoti Lalikulu la m’dziko la Argentina. Mu 1979, Khotilo linasintha cigamulo cimene cinapelekedwa ku khoti laling’ono la m’dzikolo, ndipo linati: “Kupeleka cilango cimeneci, [kucotsa ana sukulu], ndi kuphwanya ufulu wa maphunzilo mogwilizana ndi malamulo a dzikoli (Mfundo ya nambala 14), ndiponso udindo wa Boma woona kuti ana onse alandila maphunzilo a ku pulaimale (Mfundo ya nambala 5).” Cipambano cimeneci cinathandiza ana a Mboni pafupifupi 1,000. Ana ena amene anafunika kucotsedwa sukulu sanacotsedwe, ndipo ana ena amene anali atacotsedwa kale monga Pablo ndi Hugo, anawalola kubwelela ku sukulu.

Wacinyamata akana kuloŵelela m’zandale ku sukulu

Mboni za Yehova zambili zacinyamata zakhalabe zokhulupilika panthawi ya ciyeso

20, 21. Kodi mlandu wokhudza Roel ndi Emily Embralinag walimbitsa bwanji cikhulupililo canu?

20 Ku Philippines. Mu 1990, Roel Embralinag,g wa zaka 9, ndi mlongo wake Emily, wa zaka 10 pamodzi ndi ana a sukulu ena a Mboni pafupifupi 66, anacotsedwa sukulu cifukwa cokana kucitila saliyuti mbendela. A Leonardo, atate ao a Roel ndi Emily, anayesa kucondelela akuluakulu a sukuluyo, koma sizinaphule kanthu. Nkhaniyo italimba, M’bale Leonardo anapeleka nkhaniyo ku Khoti Lalikulu la m’dzikolo. M’bale Leonardo analibe ndalama, kapena loya amene akanawaimila ku khoti. Banjalo linapemphela ndi mtima wonse kwa Yehova kuti awathandize. Panthawi yonseyi anawo anali kusekedwa ndi kunyozedwa ndi anzao. M’bale Leonardo anaona kuti n’zosatheka kupambana mlanduwo cifukwa cakuti sanaphunzilepo za uloya.

21 Koma mosayembekezela, M’bale Felino Ganal anaimila banjalo pamlanduwo ku khoti. Iye anali loya amene kale anali kugwila nchito ku bungwe lina la zamalamulo komanso lochuka kwambili m’dzikolo. Panthawiyi, M’bale Ganal anali atasiya kugwila nchitoyo ndi kukhala wa Mboni za Yehova. Pamene nkhaniyo inafika ku Khoti Lalikulu la dzikolo, Khotilo linaweluza mlanduwo mokomela Mboni, ndipo linalola anawo kubwelelanso ku sukulu. Apanso, anthu amene anali kufuna kuononga cikhulupililo ca anthu a Mulungu analephela.

Kusakhala Mbali ya Dziko Kumabweletsa Mgwilizano

22, 23. (a) N’cifukwa ciani takhala tikupambana milandu yambili kukhoti? (b) Kodi gulu lathu lamtendele la abale padziko lonse ndi umboni wa ciani?

22 N’cifukwa ciani anthu a Yehova akhala akupambana milandu yambili ikuluikulu? Sitimadalila thandizo la atsogoleli andale. Komabe m’maiko ndi m’makhoti ambili, oweluza amaganizo abwino akhala akutiteteza kwa otsutsa akhanza. Zimenezi zapangitsa kuti akhazikitse malamulo a dziko amene amalemekeza ufulu wa anthu. Mosakaikila, Kristu ndi amene wakhala akutithandiza kuti tipambane milanduyo. (Ŵelengani Chivumbulutso 6:2.) N’cifukwa ciani timapeleka nkhanizo ku khoti? Colinga cathu sikufuna kusintha malamulo a m’dziko. Koma colinga cathu n’cakuti tipitilize kutumikila Mfumu yathu, Yesu Kristu, popanda coletsa.—Mac. 4:29.

23 Ngakhale kuti tikukhala m’dziko limene muli mikangano ya ndale ndi cidani, Mfumu yathu, Yesu Kristu, yakhala ikudalitsa khama la otsatila ake posatenga mbali pa nkhani za ndale. Satana walephela kutigawanitsa ndi kutigonjetsa. Ufumu wa Mulungu wasokhanitsa anthu mamiliyoni ambili amene amakana kuphunzila nkhondo. Kukhala ndi gulu lamtendele la abale padziko lonse lapansi ndi cinthu camtengo wapatali, ndipo ndi umboni wosatsutsika wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila.—Yes. 2:4.

a Voliyamu imeneyi inali kuchedwanso The New Creation. Mavoliyamu a buku la Millennial Dawn m’kupita kwa nthawi anayamba kuchedwa Studies in the Scriptures.

b Kuti mudziŵe zambili zokhudza ulosiwu, onani buku lakuti Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Ayandikira, mutu 27, tsamba 184 mpaka 186.

c Pamene cigamuloco cinasitha, boma la Bulgaria linafunika kupezela nchito zina anthu amene sanali kufuna kugwila nchito za usilikali cifukwa ca cikumbumtima cao. Linafunika kuwapezela nchito zimene sizinali kuyang’anilidwa ndi asilikali.

d Kuti mumve nkhani yonse, onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 2012, tsamba 29 mpaka 31.

e Pa nthawi ya zaka 20, Mboni za Yehova zacinyamata zoposa 450 zinaikidwa m’ndende ndi boma la Armenia. Mnyamata womaliza pa gulu la Mboni zimenezi anatulutsidwanso m’ndende mu November 2013.

f M’mafayelo a ku khoti, dzina la banjali analilakwitsa kulemba.

g M’mafayelo a ku khoti, dzina la banjali analilemba molakwitsa. M’malo molemba kuti Embralinag, analemba kuti Ebralinag.

Kodi Mumaona Kuti Ufumu wa Mulungu ndi Weniweni?

  • N’cifukwa ciani anthu a Yehova satenga mbali pankhani za ndale?

  • Kodi milandu imene anthu a Mulungu apambana ku makhoti imakuphunzitsani ciani ponena za Ufumu wa Mulungu?

  • Mungasonyeze bwanji kuti mumacilikiza Ufumu wa Mulungu mokhulupilika?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani