PHUNZILO 44
Kodi Zikondwelelo Zonse Zimam’sangalatsa Mulungu?
Yehova amafuna kuti tizisangalala na moyo, ngakhale kucitako zikondwelelo nthawi zina. Kodi zikondwelelo na maholide onse zimam’sangalatsa Mulungu? Kodi tingaonetse bwanji cikondi cathu kwa Yehova pa nkhani imeneyi?
1. N’cifukwa ciyani zikondwelelo zambili sizimam’sangalatsa Yehova?
Mungadabwe kudziŵa kuti zikondwelelo zambili si zozikika pa ziphunzitso za m’Malemba, ndipo ciyambi cake n’cacikunja. Zikondwelelo zotelo zingakhale zogwilizana na cipembedzo conyenga. Komanso zingakhale zogwilizana na zamizimu, kapena zozikika pa ciphunzitso cakuti moyo sumafa. Zikondwelelo zina ni zozikika mu zamatsenga, komanso pa cikhulupililo mwa mulungu wa Mwayi. (Yesaya 65:11) Yehova amacenjeza alambili ake kuti: “Lekanani nawo, . . . Musakhudze cinthu codetsedwa.”—2 Akorinto 6:17.a
2. Kodi Yehova amaziona bwanji zikondwelelo zimene zimalemekeza anthu mopambanitsa?
Yehova amaticenjeza kusagwela mu msampha “wokhulupilila mwa munthu aliyense wocokela kufumbi.” (Ŵelengani Yeremiya 17:5.) Zikondwelelo zina zimalemekeza olamulila kapena ngwazi za nkhondo. Maholide ena amakhala okondwelela cizindikilo ca dziko lawo monga mbendela, komanso kukondwelela ufulu wa dziko lawo. (1 Yohane 5:21) Maholide ena amakondwelela magulu andale kapena olimbikitsa kusintha zinthu. Kodi Yehova angamve bwanji ngati tipeleka ulemu wopambanitsa kwa munthu kapena gulu, maka-maka limene limacita zinthu zosemphana na cifuniklo Cake?
3. Ni macitidwe ati amene angapangitse zikondwelelo kukhala zosavomelezeka?
Baibo imaletsa “kumwa vinyo mopitilila muyezo, maphwando aphokoso, [komanso] kumwa kwa mpikisano.” (1 Petulo 4:3) Pa zikondwelelo zina anthu amacita zinthu mosadziletsa komanso zinthu zoipa. Kuti tipitilize kukhala mabwenzi a Yehova, tiyenela kutalikilana na macitidwe odetsa amenewa.
KUMBANI MOZAMILAPO
Dziŵani zimene mungacite kuti mukondweletse Yehova popanga zisankho zanzelu zokhudza maholide na zikondwelelo.
4. Pewani zikondwelelo zosalemekeza Yehova
Ŵelengani Aefeso 5:10, na kukambilana mafunso aya:
Kodi tiyenela kutsimikizila za ciyani pofuna kupanga cisankho cakuti tikondwelele holide kapena ayi?
Kodi kwanuko ni maholide ati amene anthu amakondwelela?
Kodi inu muona kuti maholide amenewo amakondweletsa Yehova?
Mwacitsanzo, kodi munayamba mwaganizapo za mmene Mulungu amaonela masiku a kubadwa? Baibo sichulako wolambila Yehova aliyense amene anakondwelelapo tsiku la kubadwa. Zikondwelelo ziŵili zokha za tsiku la kubadwa zimene limachula zinali za anthu osam’tumikila. Ŵelengani Genesis 40:20-22 na Mateyu 14:6-10. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:
Kodi pa zikondwelelo za tsiku la kubadwa ziŵili izi panacitika cinthu cofanana cotani?
Malinga na nkhani za m’Baibo zimenezi, kodi muganiza Yehova amakuona bwanji kukondwelela tsiku la kubadwa?
Komabe mungadzifunse kuti, ‘Kodi zimam’khudza Yehova nikakondwelela tsiku la kubadwa kapena holide iliyonse yosagwilizana na Malemba?’ Ŵelengani Ekisodo 32:1-8. Pambuyo pake, tambani VIDIYO na kukambilana mafunso otsatila.
N’cifukwa ciyani tiyenela kutsimikizila kuti izi Yehova amazivomeleza?
Ndipo tingacite motani zimenezo?
Mafunso otithandiza kudziŵa ngati cikondwelelo cimasangalatsa Mulungu
Kodi cikondwelelo cimeneci n’cozikika mu ziphunzitso zosemphana na Malemba? Fufuzani, pezani kuti cinayambila poti.
Kodi cimapeleka ulemu wopambanitsa kwa anthu, ku magulu a anthu kapena ku cizindikilo ca dziko monga mbendela? Ife timalemekeza Yehova kuposa wina aliyense, ndipo timakhulupilila kuti iye adzacotsapo mavuto onse padziko lapansi.
Kodi miyambo yake, komanso zocitika zolowetsedwamo, zimasemphana na mfundo za m’Baibo? Tiyenela kukhalabe oyela m’makhalidwe athu.
5. Thandizani ena kulemekeza zimene mumakhulupilila
Cingakhale covuta kukana pamene ena akukunyengelelani kucita nawo cikondwelelo cimene Yehova amadana naco. Afotokozeleni moleza mtima komanso mosamala za maganizo anu pa nkhani imeneyo. Kuti muone citsanzo ca mmene mungacitile zimenezi, tambani VIDIYO.
Ŵelengani Mateyu 7:12, na kukambilana mafunso aya:
Malinga na lemba ili, kodi muyenela kuletsa wacibale wanu amene si mboni kukondwelela holide?
Kodi mungacite ciyani potsimikizila acibale anu kuti ngakhale simudzacita nawo cikondwelelo, mumawakonda ndipo ni ofunika kwambili kwa inu?
6. Yehova amafuna kuti tizikhala osangalala
Yehova amafuna kuti tizikhalako na nthawi yosangalala pamodzi na banja lathu komanso mabwenzi athu. Ŵelengani Mlaliki 8:15, na kukambilana funso ili:
Kodi lemba ili lionetsa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala?
Yehova amafuna kuti anthu ake azikhalako na nthawi yocitako maseŵela na kusangalala capamodzi. Tambani VIDIYO kuti muone umboni wa zimenezi pa misokhano ya maiko.
Ŵelengani Agalatiya 6:10, na kukambilana mafunso aya:
Kuti ‘ticitile ena zabwino,’ kodi tiyenela kukondwelela maholide?
Kodi ni kupatsa kuti kumene mungakondwele nako—kupatsa mokakamizika cifukwa ca holide, kapena kupatsa mwa kufuna kwanu?
Nthawi na nthawi, Mboni za Yehova zambili zimakonzela ana awo cocitika capadela, ngakhale kuwapatsa mphatso zimene sanaziyembekezele. Ngati muli na ŵana, kodi mungawacitileko zinthu zapadela zotani?
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Zakuti cikondwelelo ici cinayamba bwanji zilibe kanthu kwenikweni. Cofunika ni kukhala na nthawi yosangalala pamodzi na banja komanso mabwenzi.”
Nanga inu mukutipo bwanji?
CIDULE CAKE
Yehova amafuna kuti tizipeza nthawi yosangalala pamodzi na mabanja athu, limodzinso na mabwenzi athu. Iye amafunanso kuti tizipewa zikondwelelo zimene amadana nazo.
Mafunso Obweleza
Kodi ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa kuti tidziŵe ngati cikondweleloco Yehova amadana naco kapena ayi?
Kodi acibale athu komanso mabwenzi athu tingawathandize bwanji kuti atimvetse pa nkhani yokondwelela maholide?
Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizikhala na nthawi yoseŵela komanso yosangalala?
FUFUZANI
Onani zikondwelelo za maholide zimene Akhristu satengako mbali.
“N’cifukwa Ciyani Mboni za Yehova Sizimakondwelela Maholide Ena?” (Nkhani ya pawebusaiti)
Onani zifukwa zinayi zotipangitsa kukhulupilila kuti zikondwelelo za tsiku lakubadwa sizim’sangalatsa Mulungu.
“N’cifukwa Ciyani Mboni za Yehova Sizicita Cikondwelelo ca Tsiku Lobadwa?” (Nkhani ya pawebusaiti)
Onani mmene mnyamata wina anacitila mwanzelu ku sukulu pamene anzake anamuseka cifukwa ca zimene amakhulupilila pa nkhani yokondwelela Khrisimasi.
Akhristu ofika m’mamiliyoni anapanga cisankho cosakondwelela Khrisimasi. Kodi anamva bwanji pa cisankho cawo?
“Amasangalala Ngakhale Kuti Sachita Khirisimasi” (Nsanja ya Mlonda, December 1, 2012)
a Onani Mfundo yakumapeto 5 kuti mudziŵe zimene mungacite na zocitika zokhudza maholide.