Kodi Cipembedzo Mungacikhulupilile Pankhani ya Ndalama?
Estelleandi ana ake 7, nthawi zonse anali kupita kuchalichi. Iye anati: “Ndinauza abusa anga kuti ndifuna kuphunzila Baibo.” Koma io sanafune kumuphunzitsa. Patapita nthawi, Estelle analeka kupita kuchalichi. Iye ananenanso kuti: “Akulu-akulu a chalichi anandilembela kalata, ndipo mfundo yao yaikulu inali yakuti ndizitumiza ndalama ngakhale kuti sindinapite kuchalichi. Zimenezi zinandipangitsa kudziŵa kuti io analibe nazo nchito kaya ndapita kuchalichi kapena ai. Iwo anali kufuna cabe ndalama.”
Angelina, amene amakonda kupita kuchalichi anati: “Kuchalichi kwanga anali kupititsa mbale katatu panthawi iliyonse ya mapemphelo. Ndipo nthawi iliyonse anali kufuna kuti tiziponyamo ndalama. Iwo anali kufuna cabe ndalama. Zimenezi zinandipangitsa kuona kuti anthu amenewo alibe mzimu wa Mulungu.’”
Kodi kudela lanu zipembedzo zimanyengelela anthu kapena kuwakakamiza kupeleka ndalama? Kodi kucita zimenezo ndi kogwilizana ndi zimene Baibo imaphunzitsa?
ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA
Yesu amene anayambitsa Cikristu anati: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.” (Mateyu 10:8) Uthenga wa m’Baibo ndi wamtengo wapatali ndipo uyenela kupatsidwa kwa aliyense amene aufuna kwaulele.
Kodi Akristu oyambilila anali kupeza bwanji ndalama kuti asamalile zofunika za mpingo?
Munthu aliyense anali kupeleka “mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” (2 Akorinto 9:7) Mtumwi Paulo anati: “Mwa kugwila nchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipilile kanthu kalikonse pofuna kutithandiza, tinalalikila uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu.” (1 Atesalonika 2:9) Paulo anali kupanga mahema kuti adzicilikize pa utumiki wake.—Machitidwe 18:2, 3.
KODI MBONI ZA YEHOVA ZIMACITA BWANJI PANKHANIYI?
Mboni za Yehova zimacitila misonkhano yao m’nyumba zooneka bwino zochedwa Nyumba za Ufumu. Kodi ndalama zosamalila nyumba zimenezi zimacokela kuti? Iwo samapititsamo mbale kapena kutumiza maimvulupu opemphela ndalama. Koma aliyense amene amayamikila misonkhano imeneyi, amaponya copeleka cake mosadzionetsela m’bokosi la zopeleka mu Nyumba ya Ufumu.
N’zodziŵikilatu kuti pamafunika ndalama kuti magazini ino isindikizidwe ndi kutumizidwa. Koma Mboni za Yehova sizimacita malonda kapena kupempha-pempha ndalama. Nchito yao yaikulu ndi yofalitsa coonadi ca m’Baibo.
Muganiza bwanji: Kodi njila imene Mboni za Yehova zimapezela ndalama ndi yogwilizana ndi mau a Yesu, ndipo kodi amatsatila citsanzo ca Akristu oyambilila?
[Mau apansi]
a Maina ena m’nkhani zimenezi tawasintha.
[Mau okopa papeji 4]
Kodi ndalama zoyendetsela cipembedzo ziyenela kucokela kuti?