NKHANI YA PACIKUTO | MABODZA AMENE AMALEPHELETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU
Cifukwa Cake Ambili Amaona Kuti Kukonda Mulungu N’kovuta
“‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba.”—Yesu Kristu mu 33 C.E.a
Anthu ena amaona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kovuta. Iwo amaona monga Mulungu ndi wosamvetsetseka, wosaganizila ena, ndiponso wankhanza. Ganizilani mau awa amene anthu ena anakamba:
“Ndinapemphela kwa Mulungu kuti andithandize, koma ndinali kuona kuti iye ali kutali cakuti sangamve pemphelo langa. Ndinayamba kuona kuti Mulungu samasamala za ena.”—Marco, Italy.
“Ndinali kufunitsitsa kutumikila Mulungu, koma ndinaona kuti iye ali kutali kwambili ndi ine. Ndinali kuona kuti Mulungu ndi wankhanza ndipo amatilanga. Sindinali kukhulupilila kuti ndi wacikondi.”—Rosa Guatemala.
“Pamene ndinali mwana ndinali kukhulupilila kuti Mulungu amafuna-funa zolakwa mwa ife, ndipo amangofuna kutilanga tikalakwa. Pambuyo pake ndinayamba kuona kuti iye saganizila ena. Kwa ine Mulungu anali ngati wolamulila amene saganizila za mavuto a anthu amene amawalamulila.”—Raymonde, Canada.
Kodi inu muganiza kuti Mulungu ndi wotani? Kwa zaka zambili, Akristu ena akhala akukaikila kuti Mulungu ali ndi makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, m’zaka za m’ma 500 mpaka 1500 C.E, anthu ambili a m’ Machalichi Acikristu sanali kupemphela kwa Mulungu Wamphamvuyonse. N’cifukwa ciani zinali conco? Anthu anali kucita naye mantha. Katswili wolemba mbili yakale wochedwa Will Durant, analemba kuti: “N’zosatheka kuti munthu wocimwa apemphele kwa mfumu yoopsa ndi yosaganizila ena ngati imeneyo.”
N’cifukwa ciani anthu anali kuona kuti Mulungu ndi ‘woopsa ndi wosaganizila ena’? Kodi Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu ndi wotani kweni-kweni? Kodi kudziŵa zoona ponena za Mulungu kungakuthandizeni kuti muyambe kumukonda?
[Mau apansi]
[Eni Zithunzi papeji 3]
Pamwamba, utatu: Museo Bardini, Florence; pakati, helo: © Photononstop/Superstock