NKHANI YA PACIKUTO | -KODI MULUNGU MMACITA NANU CIDWI?
Kodi Mulungu Amakuŵelengelani?
“Ine ndasautsika ndipo ndasauka. Yehova amandiŵelengela,” anatelo DAVIDE WA KU ISIRAELI, ZAKA ZA M’MA 1000 B.C.E.a
Kodi zinali zomveka kuti Davide ayembekezele Mulungu kumuŵelengela? Kodi Mulungu amakuŵelengelani? N’cifukwa ciani anthu ambili zimawavuta kukhulupilila kuti Mulungu wamphamvuyonse angawaŵelengele?
Cifukwa cimodzi n’cakuti Mulungu ndi wapamwamba kwambili kuposa anthu. Akamayang’ana anthu kucokela pa malo ake okwezeka, mitundu yonse “ili ngati dontho la madzi locokela mumtsuko, ndipo kwa iye ili ngati fumbi pasikelo.” (Yes. 40:15) Mtolankhani wina anafika ponena kuti “kungakhale kudzitukumula kukhulupilila kuti kuli Mulungu amene amacita cidwi ndi zinthu zimene timacita.”
Komabe, anthu ena amaona kuti zocita zao zimacititsa kuti Mulungu asaziwaŵelengela. Mwacitsanzo, mwamuna wina wacikulile ndithu, dzina lake Jim, anati: “Nthawi zambili ndinali kupempha Mulungu kuti andithandize kukhala wamtendele ndi wodziletsa koma pakangopita nthaŵi, mkwiyo wanga unali kubwelanso. Conco ndinaganiza kuti ndinali woipa kwambili ndipo Mulungu sakanatha kundithandiza.”
Kodi Mulungu ali patali kwambili ndi anthu cakuti sangathe kutiona? Kodi anthu ake opanda ungwilo amawaona bwanji? Palibe munthu amene angalankhulile Mulungu ndi kuyankha mafunso amenewo ngati Mulungu sanatifotokozele za iye mwini. Komabe, Baibulo limene lili ndi uthenga wa Mulungu kwa anthu, limatitsimikizila kuti sali patali nafe ndipo amaŵelengela munthu aliyense payekha. Baibulo limati: “Kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:27) Nkhani zotsatila zinai, zidzafotokoza mmene Mulungu amaonetsela cidwi kwa munthu aliyense payekha ndiponso mmene wacitila zimenezi kwa anthu enieni monga inu.
a Salimo 40:17; Yehova ndi dzina la Mulungu monga mmene Baibulo limanenela.