LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp19 na. 3 masa. 14-15
  • N’zotheka Kukhala Na Umoyo Wacimwemwe Pali Pano

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’zotheka Kukhala Na Umoyo Wacimwemwe Pali Pano
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUKHALA WOSAKHUTILA
  • KUPILILA PAMENE TIDWALA
  • KULIMBITSA CIKWATI
  • Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • Zinsinsi Zotithandiza Kukhala Okhutila
    Galamuka!—2021
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 1
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Khalani ndi Banja Lolimba ndi Lacimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
wp19 na. 3 masa. 14-15
Mmodzi wa asayansi amene aonetsedwa kuciyambi, ali pamodzi na mkazi wake akuthandizana kuphika cakudya

N’zotheka Kukhala Na Umoyo Wacimwemwe Pali Pano

KUTSOGOLO, palibe amene azidzadwala, kukalamba, kapena kufa. Ndipo na imwe mungakakhale na umoyo wabwino umenewo! Koma masiku ano umoyo ni wodzala na mavuto ambili. Nanga n’ciani cingakuthandizeni kukhala na umoyo wacimwemwe? Baibo imapeleka malangizo amene angakuthandizeni pali pano kukhala na umoyo wacimwemwe, komanso wokhutilitsa. Onani ena mwa mavuto amene timakumana nawo, na mmene Baibo ingatithandizile.

KUKHALA WOSAKHUTILA

Malangizo a m’Baibo: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”—Aheberi 13:5.

Masiku ano, pali zinthu zambili-mbili zimene anthu amakamba kuti tifunika kukhala nazo. Koma Baibo imakamba kuti tifunika kukhala ‘okhutila ndi zimene tili nazo pa nthawiyo.’ Motani?

Pewani “kukonda ndalama.” Anthu amalolela kucita zilizonse, ngakhale zowononga thanzi lawo, banja lawo, maubwenzi awo, makhalidwe awo abwino, komanso kucita zinthu zodzitaila ulemu, cabe cifukwa ca “kukonda ndalama.” (1 Timoteyo 6:10) Koma kucita izi n’kulakwitsa kwambili! Cifukwa munthu wokonda cuma “sakhutila.”—Mlaliki 5:10.

Anthu ni ofunika kuposa zinthu. N’zoona kuti zinthu zakuthupi zingatithandize. Koma zinthu sizingationetse cikondi kapena kutiyamikila. Anthu cabe ndiwo angacite izi. Ndipo kukhala na “bwenzi leni-leni” kungatithandize kuti tikhale okhutila mu umoyo.—Miyambo 17:17.

TINGAPANGITSE UMOYO WATHU KUKHALA WACIMWEMWE PALI PANO, MWA KUTSATILA MALANGIZO A M’BAIBO

KUPILILA PAMENE TIDWALA

Malangizo a m’Baibo: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa.”—Miyambo 17:22.

Monga “mankhwala ocilitsa,” cimwemwe cingatithandize kupilila matenda. Koma kodi tingacite ciani kuti tikhale acimwemwe pamene tidwala?

Khalani woyamikila. Ngati tiganizila maningi za mavuto athu, “masiku onse” adzaoneka monga oipa. (Miyambo 15:15) M’malo mwake, “sonyezani kuti ndinu oyamikila.” N’zimene Baibo imakamba (Akolose 3:15) Muziyamikila zinthu zabwino mu umoyo, olo zing’ono-zing’ono. Kukhala oyamikila pa zinthu monga kukongola kwa dzuŵa pamene iloŵa, kamphepo kayeziyezi, munthu amene timam’konda akatimwetulila, zingatipindulitse kwambili.

Muzithandiza ena. Ngakhale kuti thanzi lathu si ili bwino, “kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Machitidwe 20:35) Pamene ena ayamikila kuyesayesa kwathu powathandiza, timakhala wokhutila, ndipo izi zingatithandize kusaganizila kwambili za mavuto athu. Pamene tithandiza ena kukhala na umoyo wabwino, na ife timapindula.

KULIMBITSA CIKWATI

Malangizo a m’Baibo: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” —Afilipi 1:10.

Kwa okwatilana amene sakhala na nthawi yokwanila yoceza, cimakhala capafupi mgwilizano wawo kusokonezeka. Conco, ni cinthu canzelu kwa okwatilana kuika cikwati cawo patsogolo. Ndipo aziciona kuti ni cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili mu umoyo wawo.

Muzicitila zinthu pamodzi. M’malo mocita mwekha zinthu zimene mumakonda, bwanji osapanga pulogilamu yocitila zinthu pamodzi? Baibo imati: “Awili amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Capamodzi, mungaphike cakudya, kucita maseŵela olimbitsa thupi, kumwa zozizilitsa kukhosi, kapena kucita zinthu zina zimene mumakonda.

Onetsani mnzanu wa m’cikwati kuti mumam’konda. Baibo imalimbikitsa okwatilana kukondana na kulemekezana. (Aefeso 5:28, 33) Kumwetulilana, kukumbatilana mwacikondi, kapena kupatsanako tumphatso kungalimbitse cikwati canu. Cinanso, okwatilana afunika kukhala okhulupilika, ndipo safunika kugonana na munthu wina kupatulapo mkazi wawo kapena mwamuna wawo.—Aheberi 13:4.

“N’NAONA KUTI MOYO WANGA ULI NA COLINGA.”

—Mwini nkhani: Ryoko Miyamoto wa ku Japan.

Umoyo unali wovuta kwambili. Mwamuna wanga anali kumwa moŵa mwaucidakwa, ndipo palibe amene anali kufuna kumulemba nchito. Analeka kukwanilitsa udindo wake wosamalila ana athu anayi. Olo kuti n’nali kulimbikila nchito, zinali kuoneka zosathandiza pa banja lathu. N’nadzifunsa kuti, ‘Kodi iyi ni tembelelo, kapena cilango pa macimo amene n’nacita kumbuyoku?’

Ndiyeno, wa Mboni za Yehova anagogoda pa khomo. Akumwetulila mwacimwemwe, ananiuza za Ufumu wa Mulungu na moyo wosatha. Ananipempha kuti niziphunzila naye Baibo. Posapita nthawi, n’nadziŵa kuti Mulungu aliko, ndipo ni wanzelu, wacilungamo, komanso wacikondi. N’nadziŵanso za mkhalidwe umene akufa alili, komanso kuti mavuto amene n’nali kukumana nawo sanali cifukwa ca tembelelo.

Koposa zonse, n’nayamikila kudziŵa kuti umoyo weni-weni wokhutilitsa umadalila pa kukhala paubale na Mulungu. Kudziŵa coonadi ca m’Baibo kwanilimbikitsa kwambili, kwanimasula, na kunitsitsimula. N’naona kuti moyo wanga uli na colinga.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani