Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda May-June
“Anthu ambili sadziŵa kuti Baibulo lili ndi mayankho okhutilitsa a mafunso monga awa. [Muonetseni mafunso ali kuciyambi kwa nkhani yoyamba m’magazini a Nsanja ya Mlonda ndi kuŵelenga naye 2 Timoteyo 3:16.] Magazini iyi ifotokoza mmene mungapezele mayankho m’Baibulo lanu.”
Galamukani! July
“Masiku ano anthu ambili amapanikizika ndi mavuto? Kodi inunso mumaona conco? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limanena kuti tifunika kukhala ndi maganizo oyenela tikakumana ndi zovuta. [Ŵelengani Miyambo 24:10.] Magaziniyi ili ndi mfundo zotithandiza kuti tipilile ndipo ikufotokoza zitsanzo za anthu amene akupilila mavuto osiyanasiyana.”