Ayeletsa m’sitediyamu ya Frankfurt, ku Germany, pokonzekela msonkhano wacigawo.
Makambilano Acitsanzo
●○○ ULENDO WOYAMBA
Funso: Tidziŵa bwanji kuti mavuto amene timakumana nawo si cilango cocokela kwa Mulungu?
Lemba: Yak. 1:13
Ulalo: N’cifukwa ciani timavutika?
○●○ ULENDO WOBWELELAKO WOYAMBA
Funso: N’cifukwa ciani timavutika?
Lemba: 1 Yoh. 5:19
Ulalo: Kodi Mulungu amamvela bwanji akaona kuti tikuvutika?
○○● ULENDO WOBWELELAKO WACIŴILI
Funso: Kodi Mulungu amamvela bwanji akaona kuti tikuvutika?
Lemba: Yes. 63:9
Ulalo: Kodi Mulungu adzawathetsa bwanji mavuto athu?