Thandizo kwa Akazi Omwe Acitidwa Nkhanza
“ PA DZIKO lonse, azimayi na atsikana mamiliyoni acitilidwapo nkhanza. Kodi ndinu mmodzi wa iwo? Tiyeni tione cimene cionetsa kuti Mulungu amafuna kuti mukhale wotetezeka komanso zimene adzacita pa nkhani yocitila nkhanza akazi.”
Imayamba conco nkhani ya pa jw.org ya mutu wakuti, “Zimene Baibo Imakamba pa Nkhani ya Kuteteza Akazi.” Pansi pa nkhaniyi pali linki imene mungacitile daunilodi nkhaniyi mumpangidwe wa PDF. Kenako, mungaipulinte ndi kuipinda kukhala kathilakiti ka masamba anai. Mlongo wina wa ku America, dzina lake Stacy, anati: “Ndinapulintako timathilakiti tingapo, ndipo ine ndi mlongo wina tinapita nato kunyumba yokhalako akazi amene anacitidwapo nkhanza, imene ili m’gao la mpingo wathu.”
Mzimai wina wokhala pa nyumbayo anapempha timathilakiti tina kuti atigawile kwa anthu amene amakhala pamenepo. Maiyo anapatsidwa timathilakiti tokwana 40 pamodzi ndi timakadi tolowela pa jw.org tokwana 30. Pa ulendo wina, woyang’anila nyumbayo anapempha alongowo kuti aonetse anthu okhala panyumbapo mmene phunzilo la Baibo limacitikila.
Zocitika zosangalatsa zofanana ndi zimenezi zinacitikilanso Stacy ndi alongo ena awili pamene anapita kunyumba ina kumene kumakhala akazi amene anacitidwapo nkhanza. Iwo anagawila timathilakiti tisanu, ndipo anthuwo anapempha timathilakiti tina toonjezela. Mmodzi wa ogwila nchito panyumbapo anati, “Timapepala iti tidzawathandiza kwambili akazi amene akhala pano. Anatinso, “Timapepalati n’tofunika kwambili kwa ife.” Pa nthawi ina, anthu ambili okhala panyumba yokhalako azimai amene anacitidwa nkhanza anasonkhana pamodzi kuti aone mmene phunzilo la Baibo limacitikila. Ndipo awili mwa iwo anati angakonde kupezeka pamsonkhano wampingo wotsatila.
Stacy anakamba kuti: “Ndife osangalala kwambili poona mmene anthu ailandilila nkhaniyi. Nkhaniyi mukaipulinta papepala ndi kuipinda, ndi njila yabwino yogawilako uthenga wa Ufumu kwa akazi ocitidwa nkhanza. Tinakhudzika mtima cifukwa anatilandila bwino. Tikuyembekezela mwacidwi kuona mmene Yehova adzatithandizila pamene tikupitiliza kulengeza uthenga wabwino kwa akazi amene anacitidwapo nkhanza.”