-
Levitiko 2:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ngati mukupereka nsembe yambewu yophikidwa mu uvuni, izikhala ya ufa wabwino kwambiri. Muzipereka mkate wozungulira woboola pakati, wopanda zofufumitsa, wothira mafuta. Kapena muzipereka timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta.+
-
-
Levitiko 6:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ ndi ili: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe.
-