-
Numeri 22:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Choncho akuluakulu a ku Mowabu ndi a ku Midiyani anapita kwa Balamu+ atatenga ndalama zoti akamulipire kuti awawombezere maula, komanso anamuuza zimene Balaki ananena.
-
-
Numeri 25:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 “Akhaulitseni Amidiyani ndipo muwaphe,+ 18 chifukwa akubweretserani tsoka mochenjera pokukopani kuti muchimwe ku Peori.+ Muwaphe ndithu, chifukwanso cha zochita za mchemwali wawo Kozibi, mwana wa mtsogoleri wa ku Midiyani, amene anaphedwa+ pa tsiku limene mliri unakugwerani chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”+
-