-
Numeri 26:63, 64Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
63 Awa ndi anthu amene Mose ndi wansembe Eleazara anawawerenga pakati pa Aisiraeli. Anawawerengera mʼchipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko. 64 Koma pakati pa anthu amenewa, panalibe munthu aliyense amene anali mʼgulu la anthu omwe anawerengedwa mʼchipululu cha Sinai, nthawi imene Mose ndi wansembe Aroni anawerenga Aisiraeli.+
-