-
Numeri 26:62, 63Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
62 Onse amene anawerengedwa pakati pa Alevi analipo 23,000. Amenewa anali amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita mʼtsogolo.+ Iwo sanawerengedwe limodzi ndi Aisiraeli,+ chifukwa sanafunikire kulandira cholowa pakati pa Aisiraeli.+
63 Awa ndi anthu amene Mose ndi wansembe Eleazara anawawerenga pakati pa Aisiraeli. Anawawerengera mʼchipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko.
-