-
Numeri 21:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Koma Sihoni sanalole kuti Aisiraeli adutse mʼdziko lake. Mʼmalomwake, iye anasonkhanitsa anthu ake onse nʼkupita kukamenyana ndi Aisiraeli mʼchipululumo. Anakafika ku Yahazi ndipo anayamba kumenyana ndi Aisiraeli.+ 24 Koma Aisiraeli anapha anthuwo ndi lupanga+ nʼkuwalanda dziko lawo,+ kuyambira kuchigwa cha Arinoni+ mpaka kuchigwa cha Yaboki,+ pafupi ndi Aamoni, chifukwa Yazeri+ anachita malire ndi Aamoni.+
-
-
Yoswa 12:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Awa ndi mafumu amene Aisiraeli anagonjetsa nʼkulanda madera awo kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera kuchigwa cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba konse, chakumʼmawa:+ 2 Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni ndipo ankalamulira kuyambira kumzinda wa Aroweli,+ womwe unali mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni+ komanso kuyambira pakatikati pa chigwachi, ndi hafu ya Giliyadi mpaka kukafika kuchigwa cha Yaboki, kumalire ndi Aamoni.
-