-
1 Mbiri 11:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Benaya anaphanso munthu wamkulu modabwitsa wa ku Iguputo, yemwe anali wamtali mikono 5.*+ Ngakhale kuti munthuyu anali ndi mkondo mʼmanja mwake, waukulu ngati mtengo wogwiritsa ntchito powomba nsalu,+ Benaya anapita kukakumana naye atanyamula ndodo ndipo analanda mkondowo nʼkumupha ndi mkondo wake womwewo.+ 24 Zimenezi nʼzimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iye anali wotchuka ngati asilikali atatu amphamvu aja.
-