-
2 Samueli 21:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Kenako panayambikanso nkhondo ina ku Gati ndipo kunali munthu wamkulu modabwitsa. Iye anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse, moti anali ndi zala 24. Nayenso anali mbadwa ya Arefai.+ 21 Iye ankanyoza kwambiri Aisiraeli.+ Choncho Yonatani mwana wa Simeyi,+ mchimwene wake wa Davide, anamupha.
22 Anthu 4 amenewa anali mbadwa za Arefai ku Gati ndipo anaphedwa ndi Davide ndi atumiki ake.+
-