-
2 Samueli 3:28, 29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Davide atamva zimenezi, ananena kuti: “Yehova akudziwa kuti ineyo ndi ufumu wanga tilibe mlandu wa magazi+ a Abineri mwana wa Nera mpaka kalekale. 29 Mlandu umenewu ubwerere pamutu pa Yowabu+ ndi anthu onse a nyumba ya bambo ake. Mʼnyumba ya Yowabu musadzasowe mwamuna wa nthenda yakukha kumaliseche,+ wakhate,+ wogwira ntchito yowomba nsalu,* wophedwa ndi lupanga kapena wosowa chakudya!”+
-