-
Yesaya 5:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Tsoka kwa anthu amene amatchuka ndi kumwa vinyo kwambiri,
Komanso kwa anthu amene ndi akatswiri odziwa kusakaniza mowa.+
-
Yesaya 28:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo.
Akuyenda modzandira chifukwa cha mowa.
Wansembe ndi mneneri asochera chifukwa cha mowa.
Vinyo wawasokoneza,
Ndipo akuyenda modzandira chifukwa cha mowa.
Sakuona bwinobwino ndipo akusochera,
Komanso akulephera kusankha zinthu mwanzeru.+
-
-
Hoseya 4:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Chiwerewere, vinyo wakale ndiponso vinyo watsopano
Zimalepheretsa munthu kuchita zoyenera.+
-
-
-