-
Yesaya 5:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Pa zikondwerero zawo amaimbapo azeze, zoimbira za zingwe,
Maseche ndi zitoliro ndipo amamwapo vinyo.
Koma saganizira zochita za Yehova,
Ndipo saona ntchito ya manja ake.
-
-
Yesaya 56:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 “Tabwerani! Dikirani ndikatenge vinyo
Ndipo timwe mpaka kuledzera.+
Mawa lidzakhalanso ngati lero, mwinanso kuposa pamenepa.”
-
-
Amosi 6:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 “Tsoka kwa anthu amene akukhala mosatekeseka ku Ziyoni,
Ndiponso anthu amene akuona kuti ndi otetezeka mʼphiri la Samariya.+
Anthu olemekezeka a mtundu wotchuka kuposa mitundu ina,
Amene nyumba yonse ya Isiraeli imapita kwa iwowo.
-