-
Deuteronomo 28:51Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
51 Iwo adzadya ana a ziweto zanu ndi zipatso za nthaka yanu mpaka mutawonongedwa. Sadzakusiyirani mbewu iliyonse, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ngʼombe kapena mwana wa nkhosa mpaka atakuwonongani.+
-
-
Yeremiya 37:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Choncho Mfumu Zedekiya inalamula kuti Yeremiya atsekeredwe mʼBwalo la Alonda+ ndipo tsiku lililonse ankamupatsa mtanda wozungulira wa mkate.+ Mkate umenewu unkachokera kumsewu wa ophika mkate ndipo anapitiriza kumʼpatsa mkatewo mpaka mkate wonse utatha mumzindamo.+ Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala mʼBwalo la Alonda.
-