Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • 2 Mafumu 25:3, 4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9, njala inafika poipa kwambiri+ mumzindawo ndipo anthu analibiretu chakudya.+ 4 Ndiyeno mpanda wa mzindawo unabooledwa+ ndipo asilikali onse anathawa usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo mfumu inayamba kuthawa kulowera cha ku Araba.+

  • Yeremiya 52:6, 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9,+ njala inafika poipa kwambiri mumzindawo ndipo anthu analibiretu chakudya.+ 7 Pamapeto pake, mpanda wa mzindawo unabooledwa ndipo asilikali onse anathawa mumzindawo usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo iwo anapitiriza kuthawa kulowera cha ku Araba.+

  • Ezekieli 33:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Patapita nthawi, mʼchaka cha 12, mʼmwezi wa 10, tsiku la 5 la mweziwo, kuchokera pamene tinatengedwa kupita ku ukapolo, munthu wina amene anathawa ku Yerusalemu anabwera kwa ine+ nʼkundiuza kuti: “Mzinda uja wawonongedwa!”+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani