-
Deuteronomo 28:53-57Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
53 Zikadzatero mudzadya ana anu omwe,* mnofu wa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi+ amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzakuzungulirani.
54 Ngakhale mwamuna amene ndi wachifundo komanso wofatsa pakati panu, sadzachitira chisoni mchimwene wake, mkazi wake wokondedwa ndi ana ake aamuna amene atsala, 55 ndipo sadzagawana nawo mnofu uliwonse wa ana ake aamuna amene adzawadye, popeza adzakhala alibiretu china chilichonse chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzazungulira mizinda yanu.+ 56 Ndipo mkazi amene anakulira moyo wofewa komanso wachisasati pakati panu, amene sanayambe waganizapo zopondetsa phazi lake pansi chifukwa chokulira moyo wofewa, sadzamvera chisoni mwamuna wake wokondedwa,+ mwana wake wamwamuna komanso mwana wake wamkazi. 57 Iye sadzafuna kugawana nawo zotuluka mʼmimba mwake pambuyo pobereka komanso mnofu wa ana ake aamuna amene wabereka, popeza adzawadya mobisa chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzazungulira mizinda yanu.
-
-
2 Mafumu 25:3-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9, njala inafika poipa kwambiri+ mumzindawo ndipo anthu analibiretu chakudya.+ 4 Ndiyeno mpanda wa mzindawo unabooledwa+ ndipo asilikali onse anathawa usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo mfumu inayamba kuthawa kulowera cha ku Araba.+ 5 Koma asilikali a Akasidi anayamba kuthamangitsa mfumuyo ndipo anaipeza mʼchipululu cha Yeriko. Zitatero asilikali onse a mfumuyo anabalalika nʼkuisiya yokha. 6 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo+ nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo ndipo anaipatsa chigamulo. 7 Iwo anapha ana aamuna a Zedekiya iye akuona, kenako Zedekiyayo anamʼchititsa khungu. Atatero anamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo.+
-
-
Yesaya 3:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Tamverani! Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,
Akuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda zinthu zonse zofunika pa moyo,
Monga mkate ndi madzi.+
-